John Cena afika pa nsanja ali chifupifupi bwamuswe

Advertisement
John Cena Malawi

Zilikotu ziliko: Anthu m’masamba a nchezo akupitilirabe kung’ung’udza kamba kosamvetsa zomwe chiphona John Cena chinapanga Lamulungu lapitali pofika pa nsanja ya mwambo wina chitangobisa ulemelero wake ndi chikalata basi.

Lamulungu lapitali pa 10 March, kunali mwambo opeleka mphatso kwa akatswiri osiyanasiyana omwe amautchula kuti Oscar Awards pa chingerezi ndipo mwambowu unachitikira ku malo otchedwa Dolby Theatre mu Hollywood, Los Angeles m’dziko la United States of America.

Chomwe chinapatsa chidwi anthu ambiri nchakuti chiphona Cena yemwe anali katswiri pa nkhani ya masewero ogwetsana, kulimbana ndi kuponyerana zibonyongo, omwe pa chingerezi amatchedwa “Wrestling”, anafika pa nsanja atangobisa malo ake obisika okha.

Pa nthawiyi, Cena yemwe pano akuchita zisudzo, amapita pa nsanjapo kuti akapeleke mphatso kwa yemwe wachita bwino pa nkhani yosoka zovala ndipo anali atanyamula invilopu yomwe inali mphatso yopita kwa ochita bwinoyo.

Kuti akafike pomwe panali chinkuza mawu, katswiriyu amayenda pang’onopang’ono komaso mokhwekhweleza miyendo yake ndipo mbali inayi anthu owonelera anali akuombera m’manja pomwe enaso anangogwira kukamwa, osakhulupilira zomwe maso nawo amaonazo.

Pakadali pano, anthu makamaka m’masambaa nchezo akupeleka maganizo osiyanasiyana pa zomwe wapanga Cena ndipo ena akuti kufika pa nsanja bwamusweku kunawonjezera chisangalalo cha anthu omwe anapita ku mwambowu.

Mbali inayi, anthu ena makamaka kuno ku mpanje ndi mayiko ena a mu Africa muno, akuti uku ndikuonjeza kwambiri ndipo ena apeleka malangizo kwa ochita zisudzo mu Africa kuti asatengere zinthu ngati zimenezi

Mwambo wa Oscar Awards, omwe umakozedwa ndi Academy of Motion Picture Arts and Sciences (AMPAS) ku United States, umakozedwa chaka ndi chaka pofuna kusangalalira anthu aluso losiyanasiyana.

Advertisement