UTM yati Chilima ndiye adzayimile Tonse Alliance mu 2025

Advertisement
Malawi President Lazarus Chakwera and vice president Saulos Chilima

Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM Patricia Kaliati wati mtsogoleri wachipanchi a Saulos Chilima ndiwo adzayimile mgwirizano wa Tonse pa zisankho za mtsogoleri wa dziko lino mu 2025.

Chipani cha UTM chati mgwirizano wawo ndi Malawi Congress Party (MCP) pa yemwe akudzaimira mgwirizano wa Tonse mu chisankho mu chikudzachi sudasinthe ndipo ‘udakali chimodzimodzi’.

Mlembi wamkulu wa UTM, Patricia Kaliati, wauza wailesi ya Capital kuti adagawana zaka zisanu kwa otsogolera aliyense ndipo kuti mfundoyi sidachitike ndi atsogoleri a zipani ziwiri zokhazi ayi koma kuti otsatira ena adavomereza.

Malingana ndi Kaliati, mgwirizanowu ukudzaimiliridwa ndi mtsogoleri wa UTM, Saulos Chilima, pa chisankho cha chaka cha mawa popeza kuti mtsogoleri wa MCP, Lazarus Chakwera wachita kale mbali yake.

Ngakhale a Kaliati anena izi, chipani cha MCP chakhale chikunena kuti a Chakwera ndi omwe adzayimile chipanichi pa zisankho za chaka cha mawa.

Akatsiwiri ena pamalamulo akhalanso akunena kuti a Chilima siololedwa kuzaimila pa zisankho za mu 2025 chifukwa akhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino kwa zaka khumi ndipo khothti lalikulu ku Malawi kuno linalamulako kuti munthu sakuyenela kukhala mtsogoleri kapena wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko la Malawi kwa zaka zoposa khumi.

Advertisement