Apolisi athila utsi okhetsa misozi kutabuka zipolowe ku mpingo wa Mibawa CCAP

Advertisement
Malawi24.com

Ku mpingo wa Mibawa CCAP omwe uli pansi pa sinodi ya Blantyre kunabuka nkangano mpingowu utakana kuyimbila maliro a membala wake ponena kuti amamwa mowa.

Malingana ndi lipoti ya MBC, abale a munthu omwalirayo komanso ena omwe amakhala mozungulira derali anayamba kugenda komanso kufuna kutentha tchalitchi cha Mibawa CCAP ponena kuti chakana mkhristu wawo.

Akuluakulu a mpingowu sanazengeleze koma kuitana apolisi kuti akakhazikitse bata pa malowa.

Mkulu owona zachitetezo ku bungwe la MBC yemwe anawona izi zikuchitika wauza MBC kuti apolisi anakaponya utsi okhetsa misonzi pofuna kubalalitsa anthu ochita zisokonezowo.

Izi zachitika patangotha masiku ochepa pomwe zipolowe zina zinachitika pa mpingo wa Zolozolo CCAP ku Mzuzu omwe uli pansi pa sinodi ya Livingstonia. Zipolowe za ku Zolozolo zinachitika chifukwa choti  makwaya ena anawaletsa kuimba pa tchalitchipo potsatira kusamvana pa nkhani ya ndalama.

Advertisement