Munabuka ndewu mkachisi wa CCAP pankhani yokhudza zachuma

Advertisement

Kunali kusinthana zibagera mkachisi wa Zolozolo CCAP yomwe uli pansi pa Livingstonia Synod ku Mzuzu kamba ka mkangano omwe unabuka pankhani wokhudza zachuma pakati pamamembala ndi akuluakulu ena ampingowu mpaka apolisi anathira utsi okhetsa misonzi kukhazikitsa bata.

Nkhani yonse ikuti anthu omwe amayimba mkachisimu adawuzidwa kuti azipereka ndalama yokwana 35,000 akafuna kutenga nawo mbali.

Koma angakhale kuti oyimbawa akhala akupereka ndalamayi, yakhala isakuwoneka bwino momwe imayendera.

Izi zinapangitsa oyimbawa kufuna kudziwa momwe ndalamayi imayendera ndipo lero ananyamula mapepala amadandaulo awo ponyasidwa ndi zomwe zimachitikazi.

Iwo amafuna kuti akuluakulu a mpingo akawauze tsatanetsatane wamomwe ndalamayi ikuyendera.

Izi zinachititsa kusamvana pakati pa akuluakulu ampingowu ndi oyimbawa mpaka kufika posintha zibakera mkachisimo

Mkanganowu utakula, apolisi anabwera kudzakhazikitsa bata pothira utsi okhetsa misonzi.

Ndipo malipoti akuti anthu omwe avulala pandewuyi athamagira nawo kuchipatala.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement