Mayi wamangidwa pophwanya paipi yamadzi kuti atunge awulele

Advertisement

Apolisi ku Limbe mu mzinda wa Blantyre, akusunga m’chitokosi mzimayi wina wa zaka 21 chifukwa choononga paipi ya madzi a Blantyre Water Board mwadala ndicholinga choti atunge madzi aulele.

Malingana ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Limbe a Aubrey Singanyama, mzimayi oganizilidwayu wazindikilidwa ngati a Celina Ganya omwe akuti anapalamula mlanduwu Lachiwiri sabata ino pa 5 March, 2024 ku Bangwe munzindawu.

A Singanyama ati usiku wa Lolemba pa 4 March, 2024, paipi ina ya Blantyre Water Board idasweka kotelo kuti madzi ankatuluka ndi kumangotayika zomwe zinapangitsa anthu okhala mdelari kuti azitunga madzi aulele kudzera pa paipiyi.

Lachiwiri chakumasana munthu wina wakufuna kwa bwino, anakoza paipi yoswekayo kotelo kuti madzi anasiya kutuluka zomwe zinakwiyitsa mayi Ganya omwe kenaka anaphwanyaso mwadala paipiyo kuti apitilirebe kutunga madzi aulerewo.

Anthu ena anatsina khutu akuluakulu a Blantyre Water Board za nkhaniyi omwe sanachedwe koma kukatula nkhaniyi m’manja mwa apolisi yakudera (vakabu), omwe sanachedwe koma kumanga mayi Ganya ndikukawasiya ku polisi ya Bangwe komwe akusungidwa pano.

Celina Ganya yemwe ndiochokera m’mudzi mwa Ganya, mfumu yaikulu Ganya m’boma la Ntcheu, akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu owononga katundu.

Advertisement