Chipatala cha mpingo wakatolika cha Pirimiti achitseka

Advertisement
Malawi health workers

Chipatala cha mpingo wakatolika cha Pirimiti mu Boma la Zomba achitseka potsatira kusamvetsetsana komwe kulipo pakati pa ogwira ntchito ndi akuluakulu atatu woona ntchito zapachipatalachi.

Malinga ndichikalata chomwe Malawi24 yawona ndipo chasayinidwa ndi wapampando wa bhodi ya chipatala cha Pirimiti Dr Raphael Piringu, izi zachitika potsatira nkumano omwe akuluakulu oyendetsa chipatalachi adali nawo pa 14 December chaka chatha pomwe adagwirizana zotseka chipatalachi mpaka mtsogolo muno.

Chikalatachi chati odwala onse omwe akulandira thandizo lamankhwala pa chipatalachi akuyenera kutumidzidwa ku zipatala zina kuti adzikalandira thandizo.

Akulu akulu oyendetsa chipatala cha Pirimiti achenjeza ogwira ntchito onse kuti kuyambira pa 29 February asapezekenso akuyendayenda pachipatalachi.

Koma podandaula ndinkhaniyi, m’modzi mwa anamwino pachipatalachi yemwe sadafune kuti timutchule dzina wati zomwe achita akulu akulu oyendetsa ntchito za chipatala cha Pirimiti ndikupanda umunthu popeza chimasamalira anthu optilira 40,000 ndipo uku ndikuphwanya ufulu okhala ndi moyo wamunthu.

Iye wati ogwira ntchito pachipatalachi adzidzimutsidwa ndimaganizowa popeza sadawapatsa chenjezo lina lililonse asadabwere ndichiganizochi.

Ogwira ntchito pa chipatala cha Pirimiti miyezi yapitayi adachita ziwonetsero zosakondwa ndimomwe akulu akulu atatu (hospital administrators) amagwilira ntchito zawo ndipo adapempha kuti atatuwa awatsamutse pachipatalachi.

Advertisement