Wa polisi wanjatwa kamba koba foni ya mlonda

Advertisement

Wa polisi wa zaka 41 ku Ulongwe m’boma la Machinga ali m’manja mwa apolisi anzake kamba kakuba lamya ya m’manja ya mlonda wina.

Malingana ndi lipoti lochokera pa polisi ya Liwonde m’boma la Machinga, omangidwawa ndi Constable Blessings Patrick omwe amagwira ntchito pa polisi yaing’ono ya Ulongwe ndipo akuti achita ukathyaliwu kumayambiliro a sabata ino.

Nkhaniyi ikuti wosungitsa chitetezoyu tsiku lina sabata ino anabwereka lamya ya m’manja ya mtundu wa Techno Spark 8 yomwe akuti mwini wake ndi mlonda wina wa pa sitolo za bungwe logulitsa mbewu la ADMARC ku Ulongwe m’boma lomweli.

Wapolisiyu yemwe zikusonyesa kuti pa nthawiyi analibe foni ngakhale yothabwanya, anabweleka lamya ya mlondayu ati ndicholinga choti agwilitse ntchito kuyimbira m’chimwene wake yemwe amakhala ku Zomba.

Koma chodabwitsa nchakuti mkuluyu sanabwelele kuti akabweze lamya yobwelekayo mpaka panadutsa masiku awiri zomwe zinadabwitsa mwini lamyayi ndipo atakamufikira nkuluyu, samayankha zogwira mtima zomwe zinamupangitsa kukasiya nkhaniyi m’manja mwa apolisi a pa Liwonde.

Atalandira za nkhaniyi, apolisi a Liwonde sanazengeleze koma kumusaka oganizilidwayu ndipo atachita chipikishen, anapeza kuti a Patrick anali ndi lamya ina yaying’ono yomwe ikuganizilidwanso kuti ndi yobedwa ndipo sizikudziwika kuti lamya ya mlondayo achita nayo chiyani.

Constable Patrick yemwe amachokera m’dera la mfumu yayikulu Chilewe m’boma la Dowa, akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu wakuba.

Advertisement