Akakhala ku ndende kwa zaka zitatu kamba kochitira nkhanza mwana omupeza

Advertisement

Bwalo la majesitireti m’boma la Mangochi lagamula Martha Victor a zaka 32 zakubadwa kukhala ku ndende kwa zaka zitatu chifukwa chovulaza mwa omupeza kamba koti anakodzera nyumba.

Malinga ndi mboni ya boma, Ted Namaona wati mayi victor anakwatirana ndi bambo wa mwanayi zaka zinayi zapitazo ndipo bamboyu amagwira ntchito m’boma la Chiradzulu kotero amayendera banja lake pakatha sabata ziwiri mwezi uliwonse.

Iwo anafotokoza: “bamboyu atayendera banja lake pa 6 February, 2024, anapeza mwana wake ali mu ululu ndipo nkhope yake inali yotupa, maso ake atada komaso zipyera manja mwake.

“Atafunsa mwanayu, anafotokoza kuti mai ake omupezawa amamchitira nkhanza kwambiri bambo ake akachoka ndipo pa tsikuli ataona kuti wakodza mu nyumba, anamukalipira komaso kumenyetsa ku khoma la nyumba”

Mu nau ake Martha amene wapezeka olakwa pa mulanduwu anapempha khothi kuti limchepesere chilango kamba koti ali ndi mwana wa zaka zitatu.

Koma izi sizinakhondwerese mkulu ozenga milanduwu, Muhammad Chande, ndipo wagamula kuti mayiyu akakhale ku ndende kwa zaka zitatu kuti asinthe khalidwe lake.

Victor ndi ochokera mudzi wa Mtalika, mfumu yaikulu Chiponde m’boma la Mangochi.

Wolemba: Peter Mavuto

Advertisement