Palibe yemwe afe ndinjala – atelo a Chakwera

Advertisement
Malawi President Lazarus Chakwera accused of lying

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera watsimikizira mtundu wa a Malawi kuti palibe ngakhale munthu m’modzi yemwe amwalire chifukwa cha njala yomwe yafika posauzana m’madera ambiri m’dziko muno.

A Chakwera amayankhula izi Lachitatu pa 21 February, 2024 pomwe anakaonekera m’nyumba ya malamulo momwe anapita kukayankha mafuso okhudza zinthu zosiyanasiyana makamaka zomwe zikukhudza miyoyo ya a Malawi.

Poyankhapo pa nkhani ya chiopsezo choti anthu ambiri atha kumwalira chifukwa chosowa chakudya, nzika yoyamba ya dziko linoyi yatsindika kuti palibe ngakhale munthu m’modzi yemwe amwalire ndi njala ponena kuti boma lawo lili kalikiliki kupereka chithandizo kwa a Malawi onse omwe akhudzidwa ndi vutoli.

Iwo mwachitsazo anatchula ntchito yogawa chimanga kwa anthu omwe ali pachiopsezo cha njalayi ngati imodzi mwa zinthu zomwe boma lawo likuchita pofuna kuthana ndi vutoli ndipo ati kufika pano anthu okwana 798,319 afikilidwa ndi chakudya chomwe boma lawo likugawa.

Kupatula apo, mtsogoleri wa dziko linoyu wati posachedwapa akhala akukhazikitsa ntchito yomwe akuyitchuli mu chingerezi kuti ‘Presidential Initiative to End Hunger’ yomwe akuti cholinga chake ndi kupeleka thandizo la chakudya kwa maanja omwe akhudzidwa ndi vuto la kusowa kwa chakudya.

“Aphungu ambiri afotokoza kukhudzidwa ndi ng’amba yomwe yakhudza dziko lino yomwe ikupeleka chiopsezo cha kusowa kwa chakudya pomwe anthu opitilira 4 miliyoni akhudzidwa kale ndi njala tikukamba pano. Ndikuthokoza aliyese yemwe wayankhula pa nkhani iyi. Ndikufuna ndifotokoze kuti boma langa likudziwa za vutoli ndipo ngakhale kuti vutoli ladza kamba ka kusintha kwa nyengo zomwe ife sitingachite kanthu, boma langa likudzipeleka kupeleka chithandizo kwa a Malawi okhudzidwa ndicholinga choti pasapezeke m’Malawi yemwe amwalire chifukwa cha njala.

“Pa chifukwa chimenecho, ndine okondwa kunena kuti tikumalizitsa zokozekera pa chilinganizo chofuna kukhazikitsa ndondomeko ya mtsogoleri wa dziko pofuna kuthetsa njala (Presidential Initiative to End Hunger), ndipo tapeza kale zikwi zikwi za matumba a ufa omwe ugawidwe ku maanja omwe akhudzidwa ndi njala mdziko muno kufikira pomwe banja lili lonse likhale ndi chakudya chokwanira,” atelo a Chakwera.

Mtsogoleri wa dziko linoyo, watiso kupatula apo, pakadali pano anthu okwana 783,013 akupindula nawo mu ndondomeko ya ntukula pa khomo komaso wati boma lake lipereka zida zothandizira alimi ang’onoang’ono kuti achite ulimi wamthirira mbewu yomwe ili m’munda pano ikangokololedwa.

A Chakwera adatsegula msonkhano wanyumba yamalamulo Lachisanu pa 9 February, 2024 ndipo nkumanowu ndiokambirana za ndondomeko ya za chuma ya 2024/2025.

Advertisement