Mayi wa zaka 34 akakhala ku ndende zaka 14 kamba kogwililira mwana

Advertisement

Gladys Mtenje yemwe ndi wa zaka 34 amulamula kukakhala ku ndende zaka 14 kamba kogwililira mnyamata wa zaka 17 kwa Kauma ku Lilongwe.

Mayiyu adapalamula mlanduwu pa 1 February chaka chino.

Pa tsikuli, a Mtenje anapita kukacheza ndi mayi ake a mwanayo ku nyumba kwawo.

Apa mwanayu anali akuwerenga za kusukulu.

Patapita nthawi, mayi a mnyamatayo anachokapo kuwasiya a Mtenje omwe anapeza mpata onyengelela mwanayo kuti agone nawo.

Mayiyu adamangidwa ndi a polisi ndipo mu khothi anavomela mlanduwu.

Dzulo, bwalo pamodzi ndi apolisi a Lingadzi anapita kwa Kauma komwe bwalo linakapereka chigamulo chake.

Oweruza milandu a Rodrick Michongwe anati mayiyu anayenela kukakhala kundende moyo wake onse koma achepetsa chilangochi chifukwa a Mtenje adavomera mlanduwu mosavuta.

Nthawi yomwe bwalo limapereka chigamulo chake, anthu a m’derali anawapatsidwa mwayi oti afunse mafunso aliwonse okhudza milandu yogwilira, kugonana mokakamiza komanso kugona ndi ana.

Khothi linachita izi pofuna kupereka phunziro kwa ena.

Advertisement