Anjatidwa kamba kozembetsa matumba 124 a chimanga ku ADMARC


Apolisi m’boma la Nkhotakota amanga mkulu wa za malonda ku Chidewe  ADMARC, Patrick Duston wa zaka 35,  pomuganizira kuti ndi amene anazembetsa matumba 124  achimanga a ndalama zomwana 7.3 miliyoni.

Mneneri wa apolisi ya Nkhunga, Andrew Kamanga, wati apolisi analandira lipoti kuchokera ku likulu la ADMARC chigawo chapakati pa 10 February, 2024.

“Lipoti likutsindika kuti pa 10, February, 2024 a Duston anafufuzidwa ndipo analephera kupereka ndalama zokwana 7.3 miliyoni za matumba a achimanga okwana 124” kuyankhula Kwa Kamanga.

Patrick Duston ndi ochokera mudzi wa Makalukwa boma la Zomba ndipo akuyembekezera kukaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mulandu ozembetsa ndi kuba katundu wa boma zomwe ndi zosephana ndi gawo 238 la malamulo adziko lino.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.