Bwalo la milandu ku Zomba lapeza olakwa bambo ofuna kugulitsa mwana omupeza


Bwalo la milandu ku Zomba lapeza olakwa bambo wina Chimwemwe Zololo yemwe amafuna kugulitsa mwana omupeza kwa bambo wina ochita malonda ndipo lati lidzapereka chigamulo chake pa 14 February.

Wa Police oyimila Boma pa milandu Assistant Superintendent Peter Njiragoma adabweretsa mboni zitatu ndipo yemwe adayamba kuperekera umboni ndi Marita James yemwe ndi mkazi wake wa yemwe akuyimbidwa mulanduyi.

James adawuza bwalo kuti adawuziwa ndi amuna awo kuti agulitse mwana ati chifukwa cha umphawi.

Mboni yachiwiri adali Anold Chimenya yemwe amachita malonda ndipo iye adauza bwalo kuti adayimbilidwa phone ndi Chimwemwe Zololo kuti anali mwana wazaka ziwiri wogulitsa.

Ndipo adati atalandira foniyo adayimbira a police kuwadziwitsa zankhaniyo.

Mboni yachitatu adali wa Police ofufufuza milandu yawupandu pa police unit ya Kachulu Sub Inspector Mumba ndipo iye adauza bwalo kuti adayimbilidwa foni ndi a Chimenya ya nkhani yoti akutsatsidwa malonda amwana wazaka ziwiri.

Sub Inspector Mumba adati adachita chothekera mpaka adawagwila a Zololo omwe amatsatsa malondawo.

Zitatero, bwalo lidawunikira ma umboni omwe mboni zidaperekera ndipo lidapeza kuti a Chimwemwe Zololo ndiwolakwa.

Pamenepa, yemwe akudzenga mulanduwu Senior Resident Magistrate Mercy Bonongwe wayamba wayimitsa mulanduwu mpaka pa 14 February pomwe adzapereke chigamulo chake.

Chimwemwe Zololo ali ndi zaka 25 zakubadwa ndipo amachokera mmudzi mwa Chimbalanga, mdera la T/A Chiwalo Boma la Phalombe ndipo adapalamula mulanduwu pa 27 January chaka chino.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.