Boma lachotsa mlandu wa anthu osokoneza m’dipiti wamtsogoleri


Malawi Police

Boma lalengeza kuti lathetsa mlandu wa anthu atatu omwe anawanjata kamba kosokoneza galimoto zapa m’dipiti wa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera pomwe ankakakwera ndege ku Chileka mu mzinda wa Blantyre.

Omwe amazengedwa mulanduwu ndi a Pearson Chimimba azaka 48, a Lucy Namba azaka 48 komanso a Hector Ndawala azaka 38 zakubadwa.

Anthu atatuwa anamangidwa patapita masiku angapo kutsatira pomwe anthu ena anayimitsa galimoto zapamdipiti wamtsogoleri ponena kuti ayambe kaye ndimaliro kudutsa.

Munthawiyo mkuti naye mtsogoleri wadziko lino anali pa ulendo okakwera ndege pa Chileka munzinda wa Blantyre pa ulendo wake opita mdziko la Democratic Republic of Congo.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.