Mbava zaba “carpet”, “tent” za mtsogoleri wa dziko


Malawi presidential carpets

Anthu ena omwe sakudziwika mpaka pano akuti usiku wapitawu anakadawira galimoto ya boma ndikuba katundu wina wakunyumba yachifumu koma kwa pano akuti chinsalu chofiyira chija amayendapo mtsogoleri wa dziko m’misonkhano chija, chapezeka kutchile lina.

Usiku wa Lachitatu pa 24 January, 2024 anthu ena omwe akuganizilidwa kuti ndi okuba, anakadamira galimoto ya Ku nyumba ya chifumu yomwe inanyamula katundu yemwe amakasiyidwa ku Mwanza pokozekera msonkhano omwe a Lazarus Chakwera amayenera kuchititsa Lachinayi m’bomali.

Malingana ndi chikalata chomwe nthambi ya apolisi yatulutsa chomwe wasainira ndi ofalitsa nkhani wa nthambiyi, Peter Kalaya, atsizinamtolewa akuti anapanga chipongwechi pomwe galimotoyi imadutsa pa malo otchedwa Laundi mphepete mwa nseu wa Zalewa-Mwanza nthawi ili chamma 11 koloko usiku.

Mbavazi zinaba “Red Carpet” komanso Tent za kunyumba yaboma zomwe zimagwilitsidwa ntchito ndi mtsogoleri wa dziko ndipo apolisi ati pakadali pano akufufuza anthu omwe apanga chipongwechi.

“Malawi Police Service (MPS) ikufufuza nkhani yakubedwa kwa katundu m’galimoto ya unduna wa za mayendedwe ndi mtengatenga yomwe imupita ku Mwanza kukagwira ntchito zina.

“Izi zidachitika m’mudzi mwa Laundi m’mphepete mwa msewu wa Zalewa-Mwanza M6 cha m’ma 11 koloko usiku Lachitatu pa 24 January, 2024. Izi zidakhudza galimoto ya Nissan Croner, nambala yake MG 476 AL ya undunawu,” yatelo polisi.

Malingana ndi zithuzi zomwe taona m’masamba anchezo, pakadali pano “red carpet” yomwe inabedwayiyapezeka kutchile lino moyandikira malo omwe izi zinachitikira.

Pakadali pano nthambi yapolisiyi yatsindika kuti onse omwe angagwidwe kuti ndi zomwe apanga izi, adzalandira chilango malingana ndi malamulo a dziko lino.