Amayi awiri akwidzingidwa pofuna kulowetsa ma sim card 68 ku ndende ya Zomba

Advertisement
Malawi Prison

“Hallo, ndapatsidwa ndalama yokwana K500,000 ndi m’bale wanu kuti ndikutumizileni, nde kuti ikufikeni munditumizile kaye K50,000”: Amayi awiri ochanuka m’maso adzikapatsilidwa nsima pa zenera ku polisi ya Zomba chifukwa chofuna kulowetsa ma simu kadi okwana 68 mwachinyengo ku ndende yaikulu ya Zomba.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani pa polisi ya Zomba a Aaron Chilala Malinga omwe azindikira amayi awiriwa ngati a Eliza Ali komaso a Jean Ngombe omwe amangidwa Lachitatu pa 24 January, 2024.

A Chilala Malinga awuza nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno kuti,l amayi awiriwa anabisa ma simu kadi okwana 68 munthochi zomwe anatenga ndipo akuti amafuna kukamupatsira mchimwene wawo yemwe akugwira ukayidi pa ndendeyi.

Wachiwiri kwa ofalitsa nkhaniyu wati akuluakulu oyang’anira pa ndendeyi atawachita chipikisheni amayi awiriwa, anapeza ma simu kadi akunenedwawa omwe akuoneka kuti amafuna akamupatse m’bale wawo yemwe anapita kukamuonayo.

Izi zikuchitika pomwe anthu ambiri mdziko muno akupitilirabe kudandaula kuti akuberedwa ndalama ndi atsizinantole ena omwe amawaimbira foni ndikuwapusitsa ndipo posachedwapa, bambo winanso anamukwizinga chifukwa chofuna kulowetsa ku ndendeyi ma SIM card okwana 99.

Amayiwa akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu ofuna kulowetsa ku ndende zinthu zoletsedwa.

Advertisement