Onse omwe adayimitsa galimoto zapam’dipiti wa a Chakwera afufuzidwe, yatero NAP


Bungwe la National Advocacy Platform ladzudzula khalidwe lotchingira ndi kugenda galimoto za pamdipiti wamtsogoleri wa dziko lino ponena kuti simoyo wabwino ndipo onse okhudzidwa pa mchitidwewu akuyenera kuzengedwa

Malingana ndi kalata yomwe bungweli latulutsa ndipo wasayinila ndi wapampando wabungweli a Benedicto Kondowe, yati mchitidwewu ndi oyipa kaamba kakuti izi zimayika pachiopsezo chitetezo cha mtsogoleri wadziko komanso kudzetsa mantha pakati pa anthu.

A Kondowe anafotokozanso kuti anthu omwe akukhudzidwa ndi mchitidwewu akuyenera kuti asakidwe ndipo akapezeka akuyenera kukayankha mlandu pa zankhaniyi.

Bungweli lanena izi kutsatira zomwe zidachitika la chisanu ku Ndirande pomwe anthu ena adayimitsa mdipiti wa mtsogoleri wadziko lino pomwe iye amkapita kumwambo olumbilitsa mtsogoleri wadziko la Democratic Republic of Congo (DRC) ponena kuti ayambe adutsa ndi maliro