“Kuthanakuthana pa ndale” – Ken Msonda waopsyeza DPP kuti imumva kunyung’unya


Malawi Politician Ken Msonda

A Ken Msonda omwe ndi m’modzi mwa mamulumuzana omwe awonetsedwa nsana wa njira mchipani cha DPP, akuti chipanichi chaputa mavu nkhomora ndipo waopsyeza kuti chipanichi chiyembekezere kukha madzi ponena kuti pakadali pano wakufa pa ndale sanadziwe, akuti adzimenyera nkhondo mwa mtima bii.

A Msonda ayankhula izi kudzera mu kilipi ina yomwe anthu akugawana m’masamba a nchezo ndipo kuyankhulaku kukutsatira kalata yomwe chipani cha Democratic Progressive chatulutsa usiku wa loweruka chomwe wasaina ndi olankhulira chipanichi Shadrick Namalomba chomwe chikusonyeza kuti a Msonda komanso anzawo ena monga a Kondwani Nankhumwa, Grezelder Jeffrey achotsedwa ngati mamembala a chipanichi.

Mu ma kilipi angapo omwe tsamba lino lawapeza m’masamba anchezo, Msonda wati kuchotsedwa kwa iwo komaso anzawo ena angapo mchipanichi ndizifukwa za ndale chabe osati kuti anaphwanya malamulo a chipani ndipo wati pali anthu ena awugogodi omwe akukolezera moto za kuchotsedwa kwawo nchipani cha DPP.

Mkuluyu yemwe amadziwika bwino ndikusabisa chichewa wati ndiwodandaula kuti ngakhale anapepesa kwa mtsogoleli wa chipanichi ku Mangochi posachedwapa, zikuoneka kuti kupepesa kwawo sikunaphule kanthu ndipo kunali kopanda ntchito ndipo pachifukwa chimenecho wachotsa kupepesako komaso wati aonetsetsa kuti wathana ndi onse omwe akufuna kuthana naye pa ndale.

“Atsogoleri anzanga a chipani cha DPP, mamembala ndi a Malawi nose akufuna kwa bwino, ine Hon Kenneth Chitatata Msonda pompano ndikuchotsa chipepeso chomwe ndidapereka kwa mtsogoleri wa chipanichi komanso mawu onse a omwe ndidalankhula ku Nkopola lodge ku Mangochi pa 13 December 2023 pamsonkhano wa a NGC chifukwa zikuoneka kuti chipepeso changa sichinalandilidwe ndi utsogoleri wa chipani.

“Ndinapepesa mowona mtima chifukwa cha kufuna kuti pakhale umodzi, mwatsoka kupepesa kwanga kunalandiridwa iwo atagwira mfuti kudzanja linali; Chifukwa chake ndabwereranso kumalo omenyera nkhondo pa ndale kuti ndidzipulumutse ndekha. Apa nde andimva zenizene, kuthana-kuthana pa ndale; wakufa pa ndale sanadziwike, adziwika pomwe nkhondo ikupita,” watelo Msonda.

Iwo alangiza anzawo omwe achotsedwa nawo mchipanichi kuti akuyenera kugwirana manja ndi kudzimenyera nkhondo okha kuti apulumuke pa ndale ponena kuti anthu ena achipanichi koma osati a Peter Mutharika, ndi omwe awasungira kampeni ku mphasa.

“Maganizo anga ngati Kenneth Chitatata Msonda ndi akuti; iyi ndi nkhondo, ena akufuna kutimaliza pa ndale. Tikuyenera timenyane nawo mpaka titawamalize. Pa ndale palibe kuti zatelemu tingokhala chete, ayi izi sizampingo, iyi ndi nkhondo pa ndale. Ndiye pa ndale timati ngati munthu akufuna kukumaliza pa ndale, iweyo umayenera umumalize. Ine ndiokozeka kumaliza omwe akufuna kundimaliza pa ndale,” wateloso Msonda.