A Chakwera ati zomanga zitsate ma sitandadi


Lazarus Chakwera is President of Malawi

Poyendera nyumba za a chitetezo  zomwe akuzimanga ku Mitole  m’boma la Chikwawa,   mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati Nyumba zomangidwa zikuyenera kutsata ndondomeko zabwino  zomangira kuti zizikhala zolozeka.

Polankhula m’mau awo m’mawa  wa lero, a Chakwera ayamikila ntchito yomanga nyumba za a polisi zokwana makumi atatu (30) yomwe ili mkati  m’bomali ndipo ati ntchito isamangogwiridwa mwa chiphamaso.

“Chimene ndikufuna ine mchakuti tisangogwira ntchito pongokwanilitsa kuti ntchito yagwirika pamene ntchitoyo ndi yosalozeka komanso yochititsa manyazi tiyeni Timange potsatila ma Sitandadi abwino” anatero a Chakwera.

Nyumba zokwana makumi atatu (30) zomwe zikumangidwa ku Mitole 26 ndi za apolisi a ma udindo aang’ono ndipo 6 ndi za akuluakulu.

Nyumba zokwana 10,000 za achitetezo a ku Ndende, owona za olowa ndi otuluka mdziko, Asilikali a nkhondo, komanso Asilikali a police   zikuyembekeka kumangidwa kuchokera ku ndalama za misonkho ya a Malawi kudzera ku unduna wa za malo ndi zomangamanga kutsatila kukhazikitsidwa  ntchitoyi  ku Karonga.