Inu azibambo  a COSOMA mukundisala bwanji? Wafunsa Jetu


Musician Jetu from Malawi

Jetu walira chokweza pamene bungwe la Copyright Association of Malawi (COSOMA) silidamupatseko yachipuputa misonzi pamene bungweli lapereka makobidi kwa oyimba osiyanasiyana mdziko muno ndipo iye akufunsa kuti a COSOMA akumusala bwanji?

Jetu wayankhula izi kudzera munkanema yemwe Malawi24 yaona ndipo izi ndi zomwe wafotokoza: “Eee ndikufunseni inu azibambo aku COSOMA ine ndi Jetu azanga onse mwapatsa 2 miliyoni 2 miliyoni oyimba ine osandipatsa malo mpakananso mwagulira malo, nanga ine mukundisala bwanji? Mundiuze inu a COSOMA ine ndi Jetu.”

Jetu wayankhula izi kutsatira bungwe la COSOMA litapereka ndalama kwa oyimba osiyanasiyana mdziko muno. Driemo ndi Eli Njuchi ndi omwe alandira ndalama zokwana 5miliyoni kwacha.

Omwe alandira ndalama zokwana 4 miliyoni kwacha ndi oyimba monga Gibo Pearson komanso Skeffa Chimoto. Pamene Zeze Kingstone, Namadingo, Janta, Wikise, Lucius Banda ndi Kell Kay alandira ndalama zokwana 3 miliyoni kwacha.

PaMndandanda wa ma 2 miliyoni pali oyimba monga Zonke , Great Angels Choir, Malinga, Dan Lu,  Azizi, Jay Jay Cee, Rashley, Atoht Manje.

Pamene pa ndandanda womaliza wa ma 1 miliyoni kwacha pali oyimba monga Ace Jizzy, Beejay, Gwamba , Waxy Kay, Guntolah,  Henry Czar, DNA, Billy Kaunda, Lawi, Mlaka, Suffix, Anthony Makondetsa, Ma Blacks, Avokado, Hilco, Keturah, Moses Makawa, Nesnes, Joseph Nkasa, Phyzix,  Pop Young , Walycris,  Tremour,  komanso Lay B Salima.

Wolemba: Ben Bongololo