Pomwe anthu ena amadzudzula mkulu wa ku Mulanje yemwe anatengera ku polisi nkhumba yake yomwe imakanika kufa, apolisi ati panalibe vuto kutelo ndipo alimbikitsa anthu kuti adzipita ndi nkhani zawo za mtundu uli onse adzathandizidwa bwino.
Lamulungu lapitali pa 14 January, 2024, anthu ochuluka anakhamukira pa polisi ya Mulanje kukaona nkhumba yomwe imakanika kufa pomwe a Gresham Thunga omwe anagula nkhumbayi kwa munthu wina, anayimika manja kamba koti analephera kuipha atayesera njira zonse kwa maola oposa asanu (5).
A Thunga anauza nyumba zofalitsa nkhani mdziko muno kuti iwo agwira ntchito yopha nyama kwa zaka zoposa khumi (10) koma zomwe zinachitika pa tsikuli zinawadabwitsa kwambiri ponena kuti anali asanazionepo.
Iwo anati ataopsedwa kuti nkhumbayi siyimafa ngakhale pomwe anaibaya pa khosi komaso kuithira madzi otentha kwambiri, anapanga chiganizo chopita nayo ku polisiko kuti akawaunikire zoyenera kuchita podziwa kuti nzeru zayekha anaviika nsima m’madzi. Madzulo a tsiku lomweli, munthu yemwe anawagulitsa a Thunga nkhumbayo anakwanitsa kupha chiwetocho.
Izi zitachitika, anthu ena mdziko muno makamaka m’masamba anchezo, anadzudzula a Thunga pa zomwe anapangazo ponena kuti zinali zolakwika kwambiri ndipo ena anati uku kunali kuyigwiritsa ntchito polisi molakwika.
Koma anthu atayankhula zonsezi, apolisi mdziko muno kudzera pa zomwe ayika pa tsamba lawo la fesibuku, ati palibe cholakwika chilichonse pa zomwe mkuluyu anapanga kutengera nkhumbayo ku polisi ndipo alimbikitsaso anthu ena kuti adzipita ku polisiko ndi nkhani zawo za ntundu uli onse.
“Muli ndi ufulu kubwera ndi nkhani zanu ku Police ndipo tizakuthandizani kapena kukuunikirani koyenera kupita nazo,” analemba choncho akuluakulu a polisi pa tsamba lawo la fesibuku pomwe anaika chithuzi chotsindika kuti panalibe vuto kupita ndi nkhumbayo ku polisiko.
Pa chithunzi chomwe chinaponyedwa pa tsambali, akuluakulu a Malawi Police Service alembapo kuti; “Za nkhumba ija zatha bwino! Apolisi ndi abale anu! Timathandiza ndi kuunikira mwaukadaulo pa vuto lili lonse lomwe mwakumana nalo.”
Pakadali pano anthu ena akuyamikira Malawi Police Service kamba kothandiza pa nkhani ya nkhumbayi pomwe ena akupitililabe kudzudzula kuti uku ndikutengera ntchito za nthambi yosungutsa chitetezoyi pa mgong’o.