DODMA yapereka thandizo kwa anthu okhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi ku la Dowa


Kutsatira kusefukira kwa madzi komwe kwakhudza anthu m’boma la Dowa ku Mponela, bungwe loona za ngozi zogwa mwadzidzidzi la DODMA dzulo lapereka thandizo losiyasiyana kuphatikizapo ufa, mabulangete, mabigiri, matenti, komanso nyemba.

Bungweli lapereka mabulangete okwana 139, ufa matumba okwana 37, nyemba zolemera ma kilogiramu 10 kubanja lililonse, matenti, komanso ma mabigiri okwana 37.

A Mercy Mpakule omwe ndi wamkulu oyang’anira za chitukuko mkhonsolo ya Dowa, ayamikira bungweli kamba kochita machawi popereka thandizoli ndipo ati labwera nthawi yake pamene maanja ambiri ali ku nkhongo kusowa mtengo ogwira.

A Mpakule anapitilizanso kuti apa mpoyambira chabe kotero omwe ali ndikuthekera kopereka thandizo, asazengeleze koma apite kukapereka thandizoli kudzera ku ofesi yawo ya DODMA m’bomali.

Malingana ndi a Mpakule, tsopano anthu omwe atisiya kamba ka ngoziyi ndi atatu pamene maanja 37 ndi omwe akhudzidwa ndi ngoziyi pamene nyumba ndi mbewu zakokoloka.

Pakadali pano ena mwa omwe aperekako thandizo ndi a Napoleon Dzombe omwe apereka thandizo la ufa wa phala.

Wolemba: Ben Bongololo