Anthu abwere adzafufuze okha – Zomba mental yakana kuti ogwira ntchito akumachitira nkhaza, kupha odwala misala ozunguza

Advertisement
Zomba Mental Hospital

Akuluakulu pa chipatala cha anthu odwala matenda a misala ku Zomba awuza anthu m’dziko muno kuti ali ololedwa kupanga kafukufuku wawo-wawo pa mphekesera yoti ogwira ntchito ena pa chipatalachi akumazuza mpaka kupha odwala ozunguza pa nthawi yomwe apita ku chipatalachi kukalandira thandizo.

Chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga nchakuti anthu m’masamba a nchezo akugawana nkhani yomwe munthu wina yemwe akuti amagwira ntchito ku chipatala cha anthu a misala cha Zomba, wafotokoza kuti ogwira ntchito ena pa chipatalachi akumachitira nkhaza anthu omwe apita kukalandira thandizo la mankhwala pa matenda a muubongo.

Munthu yemwe walemba nkhaniyi yemwe pakadali pano sakudziwika kuti ndindani, wafotokoza kuti ogwira ntchito pa chipatala cha Zomba Mental, amachita nkhazazi makamaka pa nthawi yomwe odwala wagwidwa pomwe amafuna kuthawa m’chipatalachi.

Wolembayo wafotokozaso kuti odwala yemwe anamwalira posachedwapa pa chipatalachi, sankadwala koma anali atamenyedwa ndi ogwira ntchito pa chipatalapa pa nthawi yomwe ankafuna kuthawa ku chipatalachi kubwelera ku mudzi kwawo.

“Mwezi watha, kunamwalira wamisala wina kuno ndipo lipoti ananena kuti amamenyana ndi anzake pomwe ndibodza, wamisalayu anamwalira atamenyedwa atamugwira. Sikuti tikamati akuthawa ndekuti amachita kuthamangisana, monga uyu anamwalirayi, anadumpha mpanda kenako ndikumafusa anthu mumanyumba oyandikana ndichipatalachi kuti angayende bwanji kupita ku Lilongwe.

“Ma staff atangotuluka anamupeza koma kunali kuponda kumaliseche ndi jombo, zinatengera abambo ena ake kubwera kuzalelesa kuti kodi mukumumenya bwanji munthu sakupanga makani mpomwe anangomumanga mkumuponya mugalimoto koma atavulala. Madzulo ake anamwalira koma lipoti linatulusidwa kuti amamenyana amisala okhaokha koma izi ndizaboza a CID anadyeseledwa koma ngati achibale angathe azafuse anthu anyumba zoyandikira azamva chilungamo,” watelo uthenga wa munthuyu omwe ukuzungulira m’masamba a nchezo.

Koma poyankhapo za nkhaniyi, mneneri wa chipatalachi a Harry Kawiya omwe anayankhula ndi tsamba lino, ati nkhanizi ndi zabodza ndipo ati sakudziwa kuti zikuchokera pati kwenikweni.

Komabe, Kawiya wavomereza kuti chaka chatha chamu November, odwala m’modzi anamwaliradi pa chipatalachi koma watsutsa mwantu wa galu mphekesera yoti munthuyu anamwalira kamba komenyedwa ndi anthu ogwira ntchito pa chipatalachi.

Iwo ati potengera kuti nawo apolisi atchulidwa kuti akukhudzidwa pa nkhaniyi, alimbikitsa anthu komaso ma bungwe osiyanasiyana kuti ali omasuka kupita ku chipatalachi ndikupanga kafukufuku wawo-wawo (independent investigation) kuti zowona zeni zeni za nkhaniyi zidziwike.

“Munthu amene walembayo akunena kuti odwala akumamenyedwa ndikuphedwa ndi ogwira ntchito pa chipatalachi komaso akuti apolisi sakufufuza za nkhaniyi kamba koti analandira ziphuphu kuti asatelo, nde ifeyo ngati chipatala tikuti; anthu komaso ma bungwe abwere adzafufuze mwaiwo okha za nkhaniyi.

“Ifeyo ngati chipatala sitingalekelele kuti ogwira ntchito amenye munthu mpaka kumupha nde nkhaniyo ndikungoyisiya choncho, kenaka ndikuwauzaso apolisi kuti asayifufuze nkhaniyi pamene munthuyo amakhala kuti anatibweretsera ndi abale ake kuti athandizike.

“Tikuona ngati kuti tikangonena kuti ndizabodza, tipeleka uthenga olakwika ku dziko, komano tipemphe kuti anthu abwere kuti adzafufuze. Apolisi atchulidwa kuti analandira ndalama kuti asafufuze nkhaniyi nde ndi chifukwa chake tikuti aliyese atha kubwera kuno kudzapanga kafukufuku wake pa nkhaniyi,” watelo Kawiya.

Advertisement