Magetsi avuta pa chipatala cha Mzimba


Escom is the supplier of electricity in Malawi

Chipatala cha Mzimba chikumagwiritsa ntchito ndalama zosachepera K800,00 pa tsiku kugula mafuta a jenereta kamba ka vuto la kuthimathima kwa magetsi pachipatalachi.

Malawi24 yapeza kuti chipatala cha chachikulu cha boma la Mzimba chikumagula malita a pakati pa 250 ndi 300 pa tsiku oyatsila jenereta.

Mwachitsanzo, pakati pa 30, December 2023 mpaka pa 1, January, 2024, chipatalachi chinagwiritsa ntchito ndalama zoposera 2,460,600 kwacha
pogula mafuta a jenereta, pomwe anthu anakhala maola 72 wopanda magetsi a Escom.

Francis Liyati yemwe amayankhulapo pa zinthu zosiyanasiyana zochitika m’dziko muno wati ndizodabwitsa kuti pomwe boma linalengeza kuti magesi asiya kuvuta anthu a m’boma la Mzimba akuvutikabe.

“Ndizomvetsa chisoni kwambiri kuti ndalama zankhaninkhani zomwe zikupita kogula mafuta kamba kavuto la magesi zikanagwira ntchito yina. Ndikuwona ngati unduna wazamagesi komanso phungu wadelari womwenso ali anduna a Jacob Hara alowelerepo chifukwa zikuwonetsa kuti vutola la magesi ku Mzimba lafika povuta kwambiri,” anatero a Liyati.

Posachedwapa amabungwe womwe asali aboma ku Mzimba mosogozedwa ndi Wapampando wawo Christopher Melele anapita ku ofesi ya Escom m’bomali ndi kuchita zokambirana kuti amve vuto la magesi lomwe tsopano lasunduka chiphinjo koma womwe akungogwirizira udindo woyang’anira ofesi ya Mzimba ya escom a Cuthbert Ngwira ndi anzawo anakanika kuyankha mafunso womwe amabungwewo amafunsa ponena kuti iwo sali wololedwa kuyankhula chilichonse.

A Melele auza Malawi24 kuti lolemba pa 8, January,2024 nthawi 10 koloko m’mawa akhala akuchita m’kumano ndi akuluakulu a escom ochokera ku ofesi ya yikulu yaku chigawo cha kumpoto.

Naye Mkulu wa Escom kuchigawo chakumpoto, Thomas Mzumara, adatsimikiza zoti akhala akukumana ndi amabungwewo, kuti awafotokozere ngati pali vuto.

Anthu ena okhudzidwa m’bomali akuganiza kuti kuzimazima kwa magetsi komwe kukuchitikaku kwadza kamba ka wogwira ntchito ena omwe akufuna kuny’azitsa boma komanso kudzetsa udani pakati pa wanthu ndi boma lawo.