‘School Days‘ yadolora a Malawi


School Days

Pomwe zafika pano, yemwe sanaonelebe kanema othyakulidwa kwathu konkuno wa ‘School Days’, akutengedwa otsalira zedi m’makwalalamu. Kanema uyu wazula mitima ya a Malawi ochuluka ndipo omwe anaphunzira sukulu zogonera konko akumangomwetulira akamaonera kwinaku akuwasimbira ana awo mazuzo a pa gologota pomwe achina Phwedo anawapititsa ma bongwe ena mu kanemayi.

Patudutsa miyezi ingapo kanema wa School Days atatulitsidwa kumayambiliro achaka chatha, kanemayu tsopano wayamba kupezeka pa makina a intaneti, pa YouTube ndipo pofika m’mawa wa Lachitatu pa 3 January, 2024 lomweso ndi tsiku lanambala 4 chiiyikileni pa YouTube, anthu oposa 157 sauzande (157,000) anali atayionera kale filimuyi.

Filimuyi yomwe nkhani yake anapanga ndi oyimba otchuka, Kendall Kamwendo, ikukamba zokhudza nkhaza komaso mazuzo osiyanasiyana omwe ophunzira a mchaka choyamba makamaka m’sukulu za sekondale zogonera komweko amakumana nawo mudzina la tizi (tease) zomwe amachitilidwa ndi ophunzira a m’makalasi ngati fomu 3 komaso fomu 4.

Mu filimu ya School Days, Philimon Chunga yemwe amatchedwaso kuti Phwedo yemwe dzina lake lenileni ndi Tumpe Mtaya, komaso Charles Ulaya yemwe dzina lake lenileni ndi Kendall Kamwendo, Zakalia Phiri yemwe ndi Inkosi Sammy Katengeza, Judith Mambo komaso Natasha Jumbe yemwe ndi Tchanjaya Mangulenje, ndi ena mwa ophunzira a fomu 4 omwe amamvetsa mabongwe nyunyunyu.

Kanemayu anafika pamnong’a pomwe Phwedo anamutengera Mphatso ku malo omwera mowa usiku ndipo mokakamizidwa Mphatso anamwa mowa komaso kusuta kanundu kenaka ataledzera yekhayekha anawona nsana wa njira kubwelera ku mahositelo kuti akagone ndipo kenaka anamuuza Richard yemwe anakumana naye panjira kuti amuthandize kukwera mpanda wa sukuluyi.

Mphatso sakanatha kukwera mpanda yekha kamba koti mowa omwe anamwa komaso chamba chomwe anasuta chimamuonetsa zizumbazumba, koma naye Richard anakana kumukweza oledzelayo mpandawo ndipo kenaka anamupatsa chimbama chomwe anaona nacho nyenyezi, kenaka anagwa pansi ndikumenyetsa mutu wake pa mwala ndipo pomwepo Mphatso anabzala chinangwa.

Richard anamenya Mphatso kamba koti akuti ankakonda kucheza ndi msungwana otchedwa Leticia (Yvonne Chanache) yemwe Richard-yo amamufuna chibwezi koma duwalo limakanitsitsa ndipo m’malo mwake linkapeleka chikondi cha nyoo kwa Mphatso yemwe anali ophunzira wa nzeru kwambiri.

Anthu ambiri omwe awonera filimuyi akuyikweza muntengo ndipo akuti pakadali pano palibeso kanema ina yojambulidwa kuno ku mpanje yomwe ingapose iyi ndipo akuti ichi nchitsimikizo choti “industry” yopanga mafilimu ikupita patsogolo kwambiri mdziko muno.

“Sikuyankhulitsa koma this is the best ever movie Malawi has produced in 2023 (iyi ndi filimu yabwino kwambiri mu 2023).  Link kuma comment nanu muoneleko. Bravo nonse. Mwakometsa,” watelo munthu wina pa fesibuku.

Mbali inayi munthu winaso wati kanema okongolayu wamukumbutsa pa dzana ponena kuti; “Ndangomaliza kumene kuonela SCHOOL DAYS movie yi eeh Mwapha ndipo yandikumbutsa ku Dedza Secondary School ndikuuzeni nkhani komanso link ya movie kuma comment ku.”

Pakadali pano, akuluakulu omwe aphika kanemayu akupempha anthu akufuna kwa bwino kuti awaponyere kangachepe kuti nawo awoneko kusintha komaso ngati chithokozo ndi chilimbikitso potulutsa kanema okomayu.