Nankhumwa, Jeffrey sakumvetsa, akamang’ala ku khothi la apilo


Kondwani Nankhumwa is politician for the Democratic Progressive Party (DPP)

A Kondwani Nankhumwa, a Grezelder Jeffrey komanso a Cecilia Chazama ati sakumvetsetsa kuti bwalo la milandu ku Lilongwe linavomeleza kusinthidwa maudindo awo mu chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP) ndipo atatuwa akagwadwa ku bwalo lamilandu la apilo kuti abwezeretsedwe m’maudindo awo.

Izi zikudza pomwe bwalo la milandu lalikulu ku Lilongwe kumapeto kwa mwezi wa December, chaka chatha, linakanitsitsa mwa ntu wa galu pempho la anthu atatuwa omwe amafuna abwezeretsedwe m’maudino awo ku chipani cha DPP ponena kuti malamulo achipani amati maudindo awowo atha kusinthidwa kudzera ku komveshoni kokha osati zomwe mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika anapanga.

Chipani cha DPP kudzera mwa a Mutharika, chinachotsa a Nankhumwa pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi mchigawo chakumwera, mmalo mwawo munalowa a George Chaponda ndipo a Nankhumwa anasankhidwa kukhala mlangizi wa a Mutharika pamodzi ndi a Chazama omwe anali mkulu wa amayi mchipanichi ndipo m’malo mwawo munalowa a Mary Thom Navicha.

Kupatula apo, mayi Jeffrey omwe anali mlembi wamkulu wachipanichi anawasankha kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani mchigawo chapakati ndipo m’malo mwawo munalowa a Clement Mwale zomwe zinakwiyitsa makosanawa ndipo anapempha khothi kuti iwo abwezeretsedwe m’maudindo awo.

Koma khothi linakana pemphero ponena kuti anthu atatuwa analephera kupititsa kukhothiko umboni oti ufulu wawo pa ndale unaphwanyidwa ndipo kupatula apo analamulidwa kupeleka ndalama zomwe zinagwiritsidwa ntchito pa mlanduwu, koma kamba koti sanakhutitsidwe atatuwa akamang’ala ku bwalo la milandu la apilo.

Mumfundo zawo, atatuwa akupitilira kutsindika kuti maudindo awo anasankhidwa kudzera pa msonkhano waukulu wa chipani mu 2018 kotelo kuti maudindowa ayeneraso kukathera ku nkumano ngati omwewo, osati kuchotsedwa ndi mtsogoleri wa chipanichi, ngati momwe Mutharika apangira pa iwo.

Malingana ndi ofalitsa nkhani wa mtsogoleri wachipanichi a Shadreck Namalomba, mbali zonse zikumana kukhothi lero Lachitatu pomwe pomwe akuyenera kuvana chimodzi.