Wanderers yaing’ono imayenera kumenya ma “finals” awiri tsiku limodzi

Advertisement
Wanderers Reserve Players

Mpira wamapazi ku Malawi: Timu yaing’ono ya Mighty Mukuru Wanderers yomwe makolo ake atuluka chakachi opanda chikho, imayenera kumenya ma “finals” awiri, ina ku Dowa ndi ina ku Machinga, Lamulungu likubwerali.

Timu ya Wanderers Reserve Lamulungu likubwerali pa 31 December, 2023 imayenera kusewera ndime yotsiliza ndi timu ya Kalonga Rovers mu chikho cha King Kabvina pabwalo la Champion ku Dowa ndipo pa tsiku lomweli ikuyeneraso kusewera ndi timu ya Ntaja United mundime yotsiliza ya Nyasa Capital Finance pabwalo la Ntaja ku Machinga.

Koma mkulu wa bungwe la Southern Region Football Association (SRFA), Raphael Humba, Humba wati sakudziwa chilichonse pa nkhani yoti Wanderers Reserve ili ndimasewero ena patsikuli ndipo pomwe amayankhula ndi nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno, waopseza kuti ngati timuyi idzalephere kufika pabwalo la Ntaja kuti isewere masewero omaliza mu chikho cha Nyasa Capital Finance, idzalangidwa.

A Humba ati china mwa chilango chomwe chidzapelekedwe ku timuyi ndi kuphatikiza chilango chosatenga nawo gawo m’mipikisano yonse yomwe bungwe lawo la SRFA limayendetsa.

Mkuluyu wati ndizodabwitsa kuti Wanderers Reserve yomwe ili pansi pa bungwe la SRFA siyinadziwitse bungweli kuti ikutengaso nawo gawo mu chikho cha 13 miliyoni King Kabvina m’boma la Dowa komaso kuti ili ndi masewero Lamulungu likubwelari zomwe wati ndikulakwitsa kwakukulu.

Poyankhulapo, mkulu wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Roosevelt Mpinganjira wati timuyi yapelekano pempho kwa oyendetsa zikho ziwirizi ndicholinga choti masewero amodzi asunthidwe ndicholinga choti timuyi ikwanitse kusewera masewero onse.

M’mawa lero, oyendetsa chikho cha King Kabvina anena kuti ndime yomaliza ya chikhochi ayisuntha kuti izamenyedwe pa 7 January kuti apatse mwayi Wanderers kuti ipite ku Machinga.

Advertisement