Awanjata kamba kothyola m’nyumba ndikubamo katundu wa K2.3 miliyoni

Advertisement

Apolisi ku Zomba amanga njonda ziwiri chifukwa chothyola m’nyumba yosungiramo katundu ya mkulu wina ochita bizinezi pamsika wa 3 Miles ndi kubamo katundu wandalama zokwana K2.3 miliyoni.

Njonda ziwirizi ndi a Thokozan Jackson a zaka 33 zakubadwa ndi a Own Luka azaka 28 zakubadwa.

Mneneri wa apolisi m’bomali a Patricia Sipiliano atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati awiriwa adachita izi pa 12 December mwezi uno.

A Sipiliano anapitiliza kufotokoza kuti njondazi zinaba  katundu osiyanasiyana monga zida za mijigo, pampu, ndi zogwirila za mijigo ziwiri. Iwo ati katunduyi ndi wandalama zokwana 2.3 miliyoni.

Apolisi  atatsinidwa khutu pa zankhaniyi sanazengereze koma kuchita kafukufuku ndikuwamanga awiriwa.

Pakadali pano njondazi zikuyembekezereka kukayankha mulandu othyola ndi kuba katundu.

A Jackson amachokera m’mudzi wa Nasawa m’boma la Zomba,  pomwe a Luka amachokera m’mudzi mwa Chide m’boma la Thyolo.

Advertisement