Amai a CWO mu Diocese ya Zomba akakhala nawo pa msonkhano wa pachaka ku Mzuzu


Catholic Church Malawi

Amai 56 a Bungwe la Catholic Women Organization (CWO) ochokera mu Diocese ya Zomba anyamuka Lachiwiri madzulo kupita ku Mzuzu Diocese komwe akukhala nawo pa msonkhano wa pachaka wa amai a Bungweli wochokera ma Diocese onse muno Malawi.

Poyankhula asadanyamuke ku Zomba Cathedral yemwe adayimilira wapampando wa bungwe la CWO mu Diocese ya Zomba Professor Ngeyi Kanyongolo adati ku msonkhanoku amai akakambirana zambiri zokhudza momwe angayendetsere bungwe lawo.

Prof Kanyongolo adatinso ku msonkhanoko akasankhanso atsogoleri atsopano omwe ayendetse bungwe la Catholic Women Organization muno Malawi.

“Tikupita ku Mzuzu Diocese ku msonkhano wa bungwe la Catholic Women Organization ndipo tikakambirana zinthu zambiri zopititsa bungwe lathu patsogolo komanso tikawunikira momwe tagwilira ntchito zathu chaka chikungothachi ndipo pamepeto azonse tikatsankha nthumwi zatsopano zomwe zitsogolere bungweli,” Adatero Professor Ngeyi Kanyongolo.

Mu mau ake Fr. Stanislas Mchenga adafunila zabwino zonse amai omwe akukayimilira Bungwe la CWO mu Zomba Diocese ndipo adapempha Mulungu kuti awatsogolere paulendo wao.