Kwatelera: khothi layimitsa konveshoni ya DPP


Chazama, Jeffrey and Dausi at the NGTC meeting where Chazama represented DPP leader Pe6ter Mutharika

Dzuwa silingalowe osakambapo za chipani cha kale cholamura cha DPP ndipo pomwe tikudikira kuti mawa chipanichi chibweretsanji, kwa lero tasiyira poti khothi lalamura kuti zonse zomwe zinakambidwa kunkumano wa NGC omwe anaitanitsa a Grezelder Jeffrey zisachitike kaye, kuphatikiza konveshoni.

Sabata yatha, a Jeffrey mwa mphamvu zawo ngati mlembi wamkulu wa chipani cha Democratic Progressive anaitanitsa nkumano wa komiti yaikulu ya chipani, NGC komwe akuti anagwirizana mfundo zingapo kuphatikizapo kuti chipanichi chichititse msonkhano waukulu komwe akasankhe ma udindo osiyanasiyana.

Akuluakulu omwe anapezeka kunkumanowu omwe zikumveka kuti sanapitilire makumi asanu (50), anakhazikitsa masiku apa 15 komaso 16 December chaka chino ngati omwe chipanichi chipangitse msonkhano wa komveshoni ndiposo a Nicholas Dausi anasankhidwa ngati wa pampando wa komveshoniyo.

Koma pomwe kwangotsala masiku ochepa kuti komveshoniyi yomwe imayembekezeka kuchitikira ku Lilongwe ichitike, gawo lina la anthu a chipanichi omwe sakugwirizana ndi nkumano wa NGC omwe a Jeffrey anaitanitsa, linakagwada ku bwalo la milandu kuti liwapatse chiletso pa mfundo zomwe zinakambidwa ku nkumano wa NGC.

Malingana ndi chikalata cha khothi chomwe tsamba lino lapeza chomwe chikusonyeza tsiku lolemba pa 11 December, 2023, mbali ya chipanichi yomwe ikufuna kuti komveshoniyi isachitike sabata ino, yakatenga chiletsochi kudzera mwa oyimilira anthu pa mlandu a Bob Chimkango ndipo oweruza Justice Simeon Mdeza wapelekadi chiletsocho.

“Pempho lidaperekedwa pa 11 December, 2023 ndi Bob Chimkango oyimilira mbali yokhudzidwa kwa Justice S. Mdeza ndipo wolemekezeka Justice S. Mdeza anamva pempholi ndipo anawerenga lumbiriro lolembedwa mu ndandanda 1 ndipo anavomera zomwe zili mu Ndandanda 2 ya lamuloli.

“Chiletso chapelekedwa kuletsa Wodandaula Wachiwiri ndi Woyimbidwa mlandu kudzera mwa iwo eni, othandizira awo, antchito kapena antchito kapena anthu ena onse omwe akuwayimira kuti asakwanilitse mfundo za msonkhano wa National Governing Council omwe unachitika pa 6 December, 2023 omwe unachitikira ku Golden Peacock Hotel, mumzinda wa Lilongwe, mpaka pamene mlanduwu udzamvedwe kapena mpaka pamene khoti lidzapereke chigamulo china,” yatelo mbali ina ya chigamulo cha chiletso.

Kupitilira apo, khothili lawopseza kuti ngati lingapeze kuti chigamulo chomwe lapelekachi sichikutsatidwa ndi mbali zokhudzidwa, lidzamanga osamverayo, kumutumiza kukaseweza jere, kulipitsidwa chindapusa kapena kulandidwa katundu wake kumene.