Wophunzira ku sukulu ya anamwino wadzipha


Ndaine Game wa zaka 42, yemwe anali mu chaka chachiwiri ku sukulu ya anamwino ya Malamulo, wadzimangilira lachisanu masana.

Apolisi m’boma la Thyolo atsimikiza za imfa ya a Game omwe amaphnzira za mankhwala ku Malamulo.

Mkulu wa apolisi, a Francis Chisoti,  wati Game wasiya kalata yofotokoza za kudziphaku. Malingana ndi a Chisoti, Game yemwe ankachokera m’boma la Chikwawa wakhala akudwala msana kuyambira 2020.

Anzake a kusukulu akuti ophunzirayu nsana umamupweteka kwambiri ndiye anangoganiza zodzipha.