A Bon Kalindo omwe ndi mkulu wa Bungwe la Malawi First omwe adakadzipereka okha ku Polisi yaku Lilongwe Lolemba atamva mphekesera zokuti a police akuwafuna kuti awamange, lero adakawonekera ku Bwalo la Principal Resident Magistrate ku Zomba.
Mu bwalo la milandu, wa Police oyimira Boma pamilandu Assistant Superintendent Llyod Kachotsa adapempha bwalo kuti lisapereke bail kwa a Kalindo popedza sadatsilidze kufufudza mulanduwu ndipo adapempha masiku asanu ndi awiri (7) kuti a Kalindo akhalebe manja mwa apolisi.
Assistant Superintendent Kachotsa adatinso akuwopa kuti a Kalindo akapatsidwa bail akasokonedza umboni popedza mboni zaboma zomwe zilipo ndi anzawonso a Kalindo.
Koma lawyer yemwe akuyimira a Kalindo pamulanduwu a Timothy Chirwa adapempha bwalo kuti lipereke bail kwa a Kalindo popeza iwo adakadzipereka okha ku Police atamva kuti akufunidwa ndi apolisi.
A Chirwa adatinso a Kalindo sangakasokoneze umboni popedza mboni za Boma zomwe zilipozo sidzidatchulidwe maina ndipo sakudzidziwa.
Iwo adati bwalo lipereke ndondomeko zoti a Kalindo akapatsidwa bail adzidzitsatira.
Koma yemwe akuwerudza mulanduwu Principal Resident Magistrate Martin Chipofya wati adzapereka chigamulo chake Lachisanu pa 8 December ngati koyenera kudzapereka bali kwa a Kalindo.
A Kalindo akuwayimba mulandu oyambitsa zipolowe paziwonetsero zomwe adachititsa pa 23 November mu mzinda wa Zomba.