Mfumu Chidzalo ya ku Dowa yadzipha

Advertisement

Mfumu Chidzalo ya m’boma la Dowa, yomwe dzina lake lenileni ndi Moffat Lamulani Mlenga wa zaka 71, yadzimangirira itakanika kubweza ndalama za anthu amene inawalonjeza kuti idzawathandiza kugula fetereza otsika mtengo.

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali, Sergeant Alice Sitima lachisanu nthawi ya 6 koloko m’mawa banja la mkuluyu linapita kumunda pomwe mfumuyi anali akugwira  ntchito zina zapakhomo.

Koma atabwelera pakhomopo, anthu a mu banjali anapeza mkuluyu atadzimangilira ku denga la nyumba yake.

A Sitima ati  kafukufuku wa a polisi wasonyeza kuti mfumuyi inatenga ndalama kwa anthu ena ndipo idawauza kuti adzagwiritsa ntchito chitupa (ID) cha mfumuyi pogula feteleza.

Koma nthawi yogula feteleza itakwana, mfumuyi idatenga chitupa chake ndikupereka kwa munthu m’modzi. Idatengaso chitupa cha mkazi wake mokuba ndikukapereka kwa munthu wina kuti agule fetereza.

Apa mfumuyi ma ID anayithera koma anthu ena omwe inawatengera ndalama amavuta kuti nawonso akufuna ma ID kapena ndalama zawo.

Dzulo pa 1 December ndi pomwe mfumuyi inganiza zongodzipha.

Moffat Lamulani Mlenga amachokera m’mudzi mwa Chidzalo mfumu yaikulu Msakambewa m’bomali.

Advertisement