Khansala wa Ntiya Ward mu mzinda wa Zomba amulumbiritsa

Advertisement
Newly elected councillor Maxwell Finiyasi has been sworn in Zomba

Khansala Maxwell Finiyasi wa Ntiya Ward mu mzinda wa Zomba tsopano amulumbiritsa pankumano wa khonsolo yonse omwe udachitika Lolemba.

Mlembi wa ku High Court ku Zomba Hellen Kachala ndiyemwe walumburitsa Khansala Maxwell Finiyasi.

Khansala Finiyasi yemwe ndi wachipani cha DPP adapambana pachisankho chachibweredza chomwe chidachitika pa 26 September mwezi watha potsatira imfa ya Khansala Ramsey Kajosolo yemwe adamwalira nkati kati mwa chaka chino.

Poyankhula ndi Malawi24 atangomulumbiritsa pa udindowu, iye walonjeza kuti ayetsetsa kugwira ntchito zachitukuko ndi wina aliyense posatengera chipani chomwe ali pofuna kutukula Ntiya Ward.

Advertisement