Mwikho! Afukula manda am’bale wawo patatha zaka zinayi

Advertisement
Afukula Manda ku Kasungu

Zina ukamva kamba anga mwala: Ku Kasungu anthu ena akuti afukula manda a m’bale wawo yemwe akuti anamwalira mosadziwika bwino zaka zinayi (4) zapitazo, ndipo anthuwo akukayikira ngati mafupa omwe awapeza alidi a munthu.

Malingana ndi zomwe tsamba lino lapeza, nkhaniyi yachitika sabata ino m’mudzi wa Ng’ombe ku Chamama mdera la mfumu yayikulu Kapelula m’boma la kasungu.

Zikuveka kuti zaka zinayi zapitazo, kudelari kunamwalira munthu mwadzidzidzi ndipo imfa yake inadabwitsa anthu ochuluka kuphatikiza akubanja, ndipo anthu akhala akuganizira kuti munthuyo anachita kuphedwa m’matsenga.

Koma chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga nchakuti m’mudzimu kwa masiku ochuluka chaka chino mwakhala mukuveka mphekesera kuti omwalirayo ali moyo.

Zikuveka kuti anthu ena akhala akuyikira umboni kuti akumakumana ndi malemuwo koma kuyankhula kapena kugwirana nawo kukumakhala kovuta kamba koti akawoneka, munkuphethira kwa diso akumasowa.

Poti anthu amamanana nsima yokha osati nkhani, mphekeselayi inakawapeza akubanja omwe anali okhudzika ndipo chikumbu mtima chawo chinawakumbutsa za momwe m’bale wawoyo anadzalira chinangwa.

Monga mizu ya kachere yomwe imakumana pansi, apa akubanjawo anakhalirana pansi ndipo anapanga chiganizo choti apeze mankhwala achikuda kuti athane ndi vuto lomwe limachitikalo.

Achibale a malemu wa anapita ku manda pa malo omwe anagoneka m’bale wawoyo ndikuyamba kufukula kuti apenye zomwe zinali m’bokosi lomwe anamuikalo, paja amati kutsutsa galu mkukumba.

Kanema wina yemwe anthu akugawana m’masamba a nchezo akuwonetsa anthuwa akuphwasula bokosi lomwe anaika m’bale wawoyo kwinaku mzibambo wina akuthira m’bokosimo zinthu za madzimadzi omwe akuwoneka kuti ndi mankhwala.

Munkukambirana kwawo, anthu omwe akuwoneka nkanemayi, akukambirana za kusakhutitsidwa kwawo ndi mafupa omwe awapeza m’bokosimo ndipo ena ati mafupawo si amunthu pamene enaso akudabwa kuti nsalu zomwe munthuyo anafunditsidwa zikuoneka zowala ngati zatsopano.

“Mutu wa munthu uwu? Mafupa a munthu amaoneka chonchi zoona? Komaso onse kungowunjikana pamodzi, aaa. Nanga mafupa akumiyendo, akumapazi apita kuti, palibepotu apa? Aaa! Mafupa kungokhala ngati a ng’ombe,” anadabwa ma mulumuzanawo.

Anthu ambiri omwe awonera kanemayi asiyidwa kukamwa kuli yasa, kusowa chonena komaso kugwidwa mantha othetsa mankhalu pomwe ena akumafusana mafuso osiyanasiyana.

Advertisement