Kusamvana kunabuka pamalo omwetsera mafuta

Advertisement
Fuel service station

Kusamvana kunabuka lero m’mawa uno pamalo ena omwetsera mafuta a Petroda pa Kamuzu Road m’boma la Salima pamene mkulu wina amakana kusuntha galimoto lake.

Mkulu wina yemwe amaonetsetsa kuti zinthu zikuyenda mwa dongosolo anapempha bwana wina kuti asunthe kaye galimoto lake, kuti ena apeze mpata odutsa kamba kakuti adayima poti mzake atha kutulukira ukira.

Bwanayo anayamba kuchita makani nati iye sangasunthe galimoto lake kamba kakuti iye wagona pa malo omwetsera mafutawo.

“Ngati ndiwe bwana waku MDF, kaya ndiwe Sajenti, kaya ndiwe wa police zimenezo ndizakuntchito kwanu pano tiyeni tipange zapano pa filing’i siteshoni, ifenso tili ndi maudindo kwathu, iwe apa tikiti yako ikuyenda ngakhale uli kuno pamene ife timadalira pa msewu apa tikiti yathu yayima,” analalata mkulu yemwe anadziperekayo.

Khwimbi lofuna kumwetsa mafuta linasonkhana kuyambira dzulo madzulo pa malopa kutsatira chigalimoto chomwe chinabwera kudzatsitsa mafuta.

Wolemba: Ben Bongololo, Salima

Advertisement