Abambo anayi amangidwa powaganizila kuti anapha mnyamata wa zaka 18

Advertisement

Apolisi m’boma la Balaka amanga abambo anayi powaganizira kuti ndiwo adachitira chiwembu komanso kupha ophunzira wa pa sukulu ya sekondale ya St.Charles Lwangwa Gift Libuda.

Ophunzirayu yemwe adali ndi zaka 18 zakubadwa adachitilidwa chiwembu pa 11 September, Chaka chomwechino pomwe adakwera galimoto la mtundu wa Toyota Sienta pa ulendo wake ochokera kwa Chiendausiku kupita ku sukulu.

Anthuwa ndi a Amos Chisale a zaka 25, a Emmanuel Banda a zaka 37, a Jingo Chilembwe a zaka 41 komanso a Chimwemwe Banda a Zaka 27

Malingana ndi mneneri wa polisi ya Balaka, a Gladson M’bumpha, zadziwikanso kuti oganizilidwawa adaphanso ndi kuba ndalama zokwana K250, 000 za wochita malonda wina, a Patrick Mashalubu, pamene adali paulendo wawo okagula zokolora kunsika wa Golomoti m’boma la Dedza.

Oganizilidwawa akawonekera kubwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mulandu okupha.

A Amos Chisale ndi ochokera m’mudzi mwa Kambadi, mfumu yaikulu Mwandira m’boma la Nkhata Bay ndipo a Chimwemwe Banda ndi ochokera m’mudzi wa Mawawa, mfumu yaikulu Mwase m’boma la Kasungu.

A Emmanuel Banda ndi ochokera m’mudzi wa Mapulanga, mfumu yaikulu Mbelwa m’boma la Mzimba pomwe a Jingo Chilembwe ndi ochokera m’mudzi wa Katapito, mfumu yaikulu Chimwala m’bola la Mangochi