Anthu ku Chiradzulu adandaula ndi mchitidwe wa chinyengo m’ma Admarc

Advertisement
People trying to buy maize at Chiradzulu Admarc

Anthu ena m’boma la Chiradzulu adandaula kuti maofisala a bungwe la Admarc akugulitsa chimanga kwa mavenda mwachinyengo.

M’modzi mwa amai pamalopa s Lanesi Liviyeli a mudzi mwa Ching’amba T/A Onga anati ma iwo omwe anati anafika pamalopa 5 koloko ndipo anawona ma ofisalawa akumalowesa mavenda kukhomo lakuseli ndikumatuluka ndi matumba a 25 kilogalamu okwana asanu m’malo mwa thumba limodzi la 25 kilogalamu.

Cassim Jali yemwe anatiso pamalopa anafikapo 6 koloko anati mzere omwe unalipo pamalowa unasokonekela pamene anthu anayamba kung’ung’uza kuti chinyengo chakula pamalowa.

Koma owona za malonda pa Admarc yi a Gladys Harry watsusa zoterizi ponena kuti iwo akumatenga amai 20 kuti agule komanso abambo 20.

Malawi24 itafika pamalowa inaona kuti panali mpungwepungwe ndithu pamene maofisala ena amakangana ndi ogula mosakhala bwino.

Malawi24 inapezaso kuti a polisi ena pamalowa akutha kugula thumba latuthu (50 kg) kusiyana ndi mulingo wake wa 25 kg.

Posachedwapa, nduna yoona ma boma ang’ono ang’ono, umodzi ndi chikhalidwe inalangiza mafumu komanso adindo ena kuti azionesesa kuti mmadera awo anthu akugula chimanga m’ma Admarc mosavuta ndi mopanda chinyengo.

Advertisement