Wapolisi wamwa magalasi ku Thyolo

Advertisement
Partner of a police officer in Malawi

Wapolisi ku Thyolo wamwa magalasi pofuna kuzipha chifukwa choti anatentha mkazi wake ndi madzi owotcha.

Wapolisiyi dzina lake ndi Constable Elson Mnyalira ndipo amagwira ku PMS G Division ku Thyolo.

Mneneri wa apolisi mchigawo cha kum’mwera kwa kumvuma, a Edward Kabango atsimikiza za nkhaniyi.

Malingana ndi Kabango, a Mnyalira anapita kumowa ndipo pobwera anakangana ndi bwenzi lawo Tumelo Banda.

Pa nthawiyi mkaziyo anali akuphika chakudya.

Apolisi akuganiza kuti a Mnyalira anatenga madzi otentha nkumuthira mu nkhosi mwa mkaziyo.

Atachita izi, wapolisiyu anatenga magalasi nkumwa pofuna kudzipha koma anthu anamupulumutsa ndipo pano ali pa chipatala cha Thyolo.

Pakadali pano wapolisiyi ali mu ululu ku Chipatala chachikulu cha Thyolo

Advertisement