Galu wa pothilira mafuta wapha mtsikana wa zaka 10

Advertisement

Mtsikana wazaka khumi wafa atalumidwa ndi galu pa malo ena omwetsera mafuta agalimoto mu mzinda wa Lilongwe.

Malingana ndi lipoti la apolisi lomwe tsamba lino lawona, mtsikanayu wazindikilidwa ngati Ellen Chawanda yemwe wakumana ndi tsokali lachiwiri pa 25 July, 2023.

Lipotili likusonyeza kuti patsikuli Ellen anali ndi mkulu wake Nellie Chaola omwe anali akuchokera mbali nde nde ya Maula ndipo anali Paul end opita ku area 46 komwe onse wa amakhala.

Lipoti la apolisili likusonyeza kuti awiri wa anafika pa malo omwetsera mafuta galimoto a Puma yomwe ili pafupi hotela ya Crossroads, galuyo anathawa m’manja mwa wachitetezo wa kampani ya Safeguard, a Mtalison Damiano, a zaka 29.

A polisi ati galuyu analibe chotchongila kukamwa choncho anayamba kumuluma Ellen ndipo ataleletsedwa anatengeledwa ku chipatala cha Bwaila komwe wakamwalira akulandira thandizo la mankhwala.

Pakadali pano apolisi amanga Damiano omwe anali ndi galuyu ndipo anthu okwiya omwe anakhamukira pa malowa, apha galuyu.

Ellen Chawanda amachokera m’mudzi mwa Masaka, mfumu yaikulu Machinjiri ku Blantyre ndipo amakhala ku area 46 mu mzinda wa Lilongwe.

Advertisement