Chakwera wabwera kudzakhala, palibe angamuchotse – Chimwendo Banda

Advertisement

Kuli kanthu konthala nchala pa zisankho za mu 2025; nduna ya za maboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda akuti timu yowina sumayichotsa mgalaundi ndipo anenetsa kuti sakuona chipani chomwe chingamugwedeze Lazarus Chakwera.

Izi zalankhulidwa lamulungu pa 18 June, 2023 pomwe akuluakulu angapo a chipani cha Malawi Congress (MCP) anachititsa msonkhano wa ndale pa sukulu ya pulaimale ya Naotcha ku Chilobwe mu mzinda wa Blantyre.

Ku msonkhanowu komwe kunafika khwimbi la anthu, kunali nduna zinayi zaboma zomwe ndi; a Ken Zikhale Ng’oma, a Richard Chimwendo Banda, a Abida Mia nduna yofalitsa nkhani a Moses Kumkuyu.

Poyankhula pamalowa, a Chimwendo Banda anati potengera ndi mmene anatulukira anthu kudzakhala nawo ku m.zsonkhanowo, nzachidziwikile kuti anthu ochuluka m’dziko muno akukondwera ndi ulamuliro wa mtsogoleri wa dziko lino, a Chakwera.

Ndunayi inati anthu ambiri mdziko muno agwa m’chikondi ndi utsogoleri wa a Chakwera kaamba koti iwo akwanilitsa malonjezo ambiri omwe analonjeza nthawi yokopa anthu pomwe dziko lino linkachititsa chisankho mchaka cha 2019 komaso chisankho cha chibweleza mu 2020.

“Pambali pa mavuto omwe tinakumana nawo, panopa takhazikika, misewu yayambika, chitukuko chayambika, zinthu zayamba kuchitika bwino, nde timu yowina sumayichotsa mgalaundi.

“Tikufuna tiwatsimikizile aMalawi kuti Chakwera alipo mpaka kalekale, ndipo atitumikira, tiona kuti zinthu zonse mpaka zitheke, koma tipitilira kukhalabe odzipeleka kwa aMalawi, owavera aMalawi, sitidzitukumula komaso sitingamanene kuti tiluza chifukwa tikudziwa kuti tikuchita bwino,” anatelo a Chimwendo Banda.

Ndunayi inati msonkhanowu unakonzedwa ndicholinga chofuna kulimbikitsa anthu amdelari omwe akuti anakhudzidwa kwambiri ndi namondwe wa Freddy chaka chino yemwe anapha anthu mazanamazana.

Apa Chimwendo Banda anati mmene zinthu zinalili ndi namondwe wa Freddy, sizobisaso kuti anthu a delari akhudzidwa kwambiri ndi njala kaamba koti ambiri minda yawo inapita ndi madzi ndipo wati anthuwa alandira thandizo losiyanasiysana kuchokera ku boma.

“Tinabweraso kudzaona mavuto ali kuno. Kuli mavuto a misewu, madzi akumwa, mavuto so amene anakula kwambiri kaamba ka namondwe wa Freddy. Ifeso timafuna tiwalimbikitse kuti tikubweretsa ma pologalamu osiyanasiyana kuphatikizapo mtukula pakhomo.

“Takambaso ndi a Habitat for Humanity omwe amamanga nyumba pa ngongole kuti ayambe kuwamangira anthu amenewa nyumba zabwino. A Chakwera akufuna kuwatsimikira anthu amenewa kuti sawasiya okha, ayenda nawo limodzi,” anaonjezera choncho Banda.

Polankhalapo, mfumu Chilobwe apempha a Zikhale Ng’oma kuti adzaimire dera la kum’mwera kwa mzinda wa Blantyre (Blantyre City South Constituency) pa udindo wa phungu wa kunyumba ya malamulo.

Mfumu Chilobwe inapitilira ndikupempha boma kuti likonze vuto la misewu mdera lawo yomwe akuti yawonongeka kwambiri ndipo yapemphaso boma kuti lipitilire kuthandizabe anthu onse omwe anakhudzidwa ndi namondwe wa Freddy mderalo.

Follow us on Twitter:

Advertisement