Lulu ndi okula mtima – JB

Advertisement

Oyimba HipHop yemwe akukhala ku America, Jolly Bro, wati akuona kuti udani wakhoswe ndi mphaka omwe wayambika pakati pa iye ndi oyimba mzake Lulu siwutherapo ponena kuti Lulu ndiokura mtima, sakufuna kugonja.

Jolly Bro yemwe anabadwa Alberto Zacharias, amayankhula izi mkati mwa sabata yatha pomwe amacheza ndi imodzi mwa kampani zopanga ndikufalitsa mauthenga pa internet, Podcast Malawi.

Zacharias yemweso amadziwika kwambiri ndi dzina loti JB anati akuwona kuti kusemphana chichewa ndi Lulu kukupitilirabe kaamba koti oyimba mzakeyo sakuonetsa mtima ogonja, ndipo watsindika kuti Lulu ndi Nkula mtima.

“Atakwera mgalimoto yomwe tinali ife, tinkati ndi munthu wa bwino. Koma ka munthu akaka kamafuna kazizionetsa ngati kofatsa koma ndikoipa amwene. Mchitidwe uwuwu ofuna kumadzionetsa ngati ofatsa, Lulu wakula nawo.

“Lulu sangagonje chifukwa akuona kuti akulakwilidwa ndiiyeyo, akumati ineyo ndamene ndikumutukwana, koma ineyo ku America kuno basi ndikangokhala nkuyamba kukamba za Lulu ndi Tay Grin? Lulu ndi okula mtima kwambiri,” watelo JB.

JB anapitilira kufotokozera omwe amacheza nawo mu kanema yemwe wajambulidwayo kuti iye sakudandaula kanthu pa udaniwu ndipo wati sakuona vuto kukhala moyo wake onse osazayankhulanaso ndi oyimba mzakeyu.

“Ineyo Lulu sinzanga, olo atapanda kudzandiyankhulitsaso moyo wanga onse palibe vuto, palibe chimene chisinthe pa moyo wanga, tinangokumana koma wina amafuna adzidzionetsa ngati wankulu komano mamuna nzako mpachulu,” anateloso JB.

JB walangiza Lulu kuti aphunzile kulemekeza komaso kukhala bwino ndi anthu ena ponena kuti munthu odzichepetsa amapita patali, osati zomwe amapanga pomaoneka ngati ofatsa koma ali njoka.

Oyimbayu waululaso kuti aMalawi ambiri ku South Bend komwe akukhala pano sakumuonera kukondwa kaamba kowulura kuti aMalawi ambiri kumeneko akukhala moyo wachimidzi.

“Anthu aku South Bend ambiri anakwiya ndipo tikunena pano ambiri sakupuma nane bwino, koma ubwino wake moyo wakuno kulibe zoopsezana ngati mmene timapangira ku Malawi kwathuko,” anaonjezera choncho JB.

JB wati ubale wake ndi Lulu unavunda pomwe Lulu anavomeleza kulepheretsedwa kwa maimbidwe omwe awiriwa amayembekezeka kuti akayimbile limodzi ndipo m’malo mwake Lulu anavomera kukaimba ndi Tay Grin.

Iye wati izi zinamukwiyitsa ndipo wati ndi zomwe zinamupangitsa kuti ayambe kusambwadza Lulu komaso omwe amamulongosolera za maimbidwe ake pomwe anali m’dziko la America mwezi watha.

Koma poti nkhonya yobwezera kuwawa, Lulu anauza nyumba ina yofalutsira mawu m’dziko muno kuti samamudziwa JB zomwe zinakwiyitsa oyimba nzakeyo ndipo pakadali pano awiriwa sakumweranabe madzi.

Follow us on Twitter:

Advertisement