Zilikoliko 2025: otsatira UTM, MCP agwebana

Advertisement

Kunali chifwilimbwiti ku maofesi a Malawi Bureau of Standards (MBS) ku Blantyre pamene anthu otsatira zipani za UTM komaso MCP zomwe zili mugwirizano wa Tonse, anawongolana manja.

Izi zachitika lero lachitatu pomwe Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera komaso wachiwiri wawo a Saulos Chilima amatsekulira maofesi atsopano a bungwe la Malawi Bureau of standards.

Pomwe atsogoleri awiriwa anafika pa malowa, anthu ena ovala zovala za makaka a MCP komaso UTM, anaoneka akugwiranagwirana makamaka ku mipando ya ku tsogolo.

Tsamba lino lapeza kuti magulu awiriwa anasemphana maganizo payemwe amayenera kukhala mipando yakutsogoloyo pomwe aliyese amafuna kutelo.

Potsatira mkanganowu, mamembala a MCP anayamba kuwononga zikwangwani zomwe anthu otsatira chipani cha UTM ananyamula, kung’amba zovala, mbendera komanso kumenya anzawowo.

Chokhumudwitsa kwambiri mchakuti, zonsezi zimachitika pamaso pa a polisi omwe anangoti kakasi kusowa chochita.

Bata linabwelera pomwe mlembi wamkulu wa chipani cha UTM a Patricia Kaliati, anathamanga kukafikira mamembala a chipani chawo, kuwapempha kuti asunge bata.

A Kaliati anauza otsatira chipani chawo kuti agonje ndikulora kuti otsatira chipani cha MCP akakhale mipando yakutsogolo yomwe amalimbilanayo.

Zonsezi zikuchitika pomwe masiku akuthera kuchitseko kuti dziko lino lichititse chisankho cha patatu mchaka cha 2025.

Pakadali pano sizinadziwike ngati mgwirizano wa Tonse uzakhale ukupitilira pomafika nthawi ya chisankhoyi.

Follow us on Twitter:

Advertisement