Mayi akuphika kwa masiku anayi osapuma

Advertisement

Zina ukamva ndithudi kamba anga mwala; pamene inu mumasamba thukuta mukangophika chipagala kwa kanthawi kochepa, mayi wina ku Nigeria walowa mu tsiku lachitatu akuphika zakudya zosiyanasiyana osapuma.

Hilda Effiong Bassey amene amadziwika kwambiri ndi dzina loti Hilda Baci, ochokela mdera la Akwa Ibom, mdziko la Nigeria, ndikatswiri pankhani za maphikidwe, ndipo atha kukuphikirani mwala inu mkususira mbamu.

Hilda Baci, lero ali mkatikati mwa tsiku lachitatu akuphika zakudya zosiyanasiyana osapuma pomwe akufuna kufufuta mbiri ya munthu yemwe anaphikapo nthawi yaitali osapuma ya mu buku la Guinness World Record.

Msungwanayu akufuna kufufuta zomwe anachita Lata Tondon m’chaka cha 2019, ku Rewa mdziko la India yemwe adakhala maola 87, mphindi 45, ndi masekondi 00 akuphika, inde osapuma.

Baci yemweso amapanga masewero komaso ndi muwulutsi wa wailesi za kanema, anayamba kuphika pa 11 May chaka chino ndipo akuyembekezeka kumaliza maola oyambilira a pa 15 May, ngati angakwanitse kutelo.

Mwambowu womwe ukuchitikira ku Amore Gardens ku Lekki, Lagos, ukufuna kuwonetsa luso la Hilda Baci lophika pogwiritsa ntchito maphikidwe osiyanasiyana amdzikolo zomwe zili ndi kuthekera koyika Nigeria pamapu apadziko lonse pa nkhani zamaphikidwe.

Pakadali pano, anzake a Hilda Baci monga Enioluwa, Seyi Awolowo, Elozonam ndi ena ambiri, akupitilira kumupatsa moto mzawoyu kumalo komwe kukuchitikira mwambowu pamene ena akumuchemelera katswiri pa maphikidweyu kudzera m’masamba a mchezo.

Follow us on Twitter:

Advertisement