Pomwe akuluakulu a kampani ya Ichocho Power Security (IPS) anali kuwunguzawunguza kuti nsuzi uzipezeka bwanji ngati kampaniyi ingalandidwe chiphaso, boma labweza ganizo lake pa nkhaniyi.
Nkhaniyi inayamba sabata imodzi yapitayo pomwe mkulu wa IPS a Yassin ‘Ichocho’ Suwedi anazijambura ndikutulutsa kanema momwe anauza a Jai Banda kuti agwira ndikusunga mokaka miza mwana wawo Tonderai.
Suwedi mwathamo anauzaso a Banda kuti adzamuonaso mwana wawo Tonderai pokhapokha avomele kuyimilira gulu lake pa pempho lawo lopita ku boma kuti gululi lizitengedwa ngati gulu la asilikari a nkhondo a dziko lino.
Izi zinakwiyitsa anthu ochuluka mdziko muno kuphatikizapo nduna ya za chitetezo cha mdziko a Ken Zikhale Ng’oma omwe analamula kuti kampaniyi ilandidwe chiphaso chake.
Koma ngakhale Ichocho Suwedi anapepesa kaamba ka zomwe anayankhulazi, boma kudzera mwa akuluakulu angapo linaitana akuluakulu a kampani ya IPS kuti akawapatse mwambo
Kumeneko zadziwika tsopano kuti chiganizo cholanda chiphaso cha kampaniyi chabwezedwa ngakhale kuti kampaniyi yapatsidwa zinthu zingapo zoti ikwanilitse mwa nsanga nsanga.
Boma kudzera kwa nduna ya za chilungamo a Titus Mvalo anati kukhulukidwaku ndikamba koti kampaniyi inalemba anthu ntchito oposa 200 ndipo laona kuti chiganizo chake chikanatha kupweteketsa anthu osalakwa podziwa kuti njobvu zikamamenyani umavutika ndi udzu..
Powonjezera, nduna ya chitetezo cha dziko, Zikhale Ng’oma, yatinso ganizo losalanda chiphasochi labweranso chifukwa uwu ndi mlandu woyamba kulembetsedwa wokhudza kampaniyo.
Pakadali pano kampaniyi yapatsidwa zinthu zisanu ndi zitatu zomwe ikuyenera kutsatira kuphatikizanso kupititsaso ku undunawu zikalata zofunsira kuyambitsidwa kwa kampaniyi pasanathe masiku asanu ndi awiri.
Boma latiso litulutsa kalata yodzudzula kampaniyi yomwe akuti ikhala kalata yoyamba komanso yomaliza yochenjeza za mlanduwo ndipo kampaniyi yauzidwaso kuti iyenera kupeza katswiri wa za malamulo kuti aziyiwunikira kampaniyi pa nkhani za malamulo.
Polankhula ndi atolankhani, Wapampando wa kampani ya Ichocho Power Security a George Kasakula yemwe adatsagana ndi Suwedi ku bwaloli adati kampaniyo ndiyokhudzidwa ndi zomwe zinachitikazo.
“Kanemayu ndi chimodzi mwazinthu zomvetsa chisoni zomwe Ichocho Power Security siimayenera kuchita ndipo tikutsimikizira dziko komanso anthu onse kuti izi sizichitikanso,” atero a Kasakula.
Kupatula nduna ziwirizi, ena mwa akuluakulu a boma omwe anapezeka pa mkumanowu ndi monga mkulu wa Malawi Police Service Merlyn Yolamu komaso akulu akulu ochokela ku Malawi Defence Force.
Follow us on Twitter: