Njoka yayikazi ili ndi maliseche achizimai – atero akatswiri

Advertisement

Pamene anthu ena pa dziko lonse lapansi akhala akutsutsana kwa nthawi yaitali ngati palidi njoka za zikazi kapena za zimuna komaso ngati za zikazizo zilidi ndi maliseche oyipangitsa kuti izimva kukoma zikamagonana, akatswiri a sayasi ku Australia apeza kuti njoka za zikazi zilinso ndi mikongo ngati anthu ndi nyama zina.

Akatswiri a sayasiwa omwe ndiochokera pa sukulu ya ukachenjede ya Adelaide mdziko la Australia, anachita kafukufuku za nkhaniyi ndipo zotsatira zake zasonyeza kuti njoka iliyose yaikazi imakhala ndi ma libida awiri omwe a kuti amapezeka chapansi pa mchira wa njokazi.

Malingana ndi a Megan Folwell omwe amatsogolera kafukufuku yemwe akatswiriwa anapanga pa njoka za zikazi, iwo anagwiritsa ntchito ukachenjede wawo kuti athetse mtsutso omwe wakhalapo kwa zilumika zochuluka, ndipo anati kafukufuku wawo anamupanga pa njoka zamitundu yokwana isanu ndi inayi (9).

Iwo ati akatswiriwa anachita kauniuni wa maliseche a njoka zazikazi zikuluzikulu ndipo ati amafuna asiyanitse ndi maliseche a njoka zazimuna ndipo apapa ndipomwe zinadziwika kuti njoka ya ikazi iliyonse ili ndi malibida awiri.

“Mu ufumu wa nyama, maliseche anyama za zazikazi amanyalanyazidwa poyerekeza ndi anyama za zimuna. Kafukufuku wathu tinamupanga pa mtsutso omwe wakhalapo nthawi yaitali kuti njoka sizimakhala ndi nkongo kapena kuti sumagwira ntchito.

“Njoka zili ndi mikongo iwiri yomwe imasiyanitsidwa ndi mnofu ndipo umabisidwa pansi pamchira. Chiwalochi chili ndi mitsempha, kolajeni (collagen) komaso maselo a magazi omwe amakhala ndi minofu yomwe imatamuka,” anatelo a Folwell.

Iwo ati kaamba kosadziwa chenicheni pankhaniyi, pang’ono ndi pang’ono anthu akhala akuvomereza kuti njoka zimagonana za zikazi kapena zazimuna zokhazokha ndipo ati anthu ena amaitenga nkhani ya maliseche a njoka za zikazi ngati mwikho.

Zotsatira za kafukufukuyu a kuti zasindikizidwa mu magazini a Royal Society B ndipo zadziwika kuti imodzi mwa mtundu wa njoka zomwe zinagwiritsidwa ntchito pa kafukufukuyu ndi Puff Adder, mtundu omweso umapezeka ku Malawi.

Tipedzeni ku Twitter

Advertisement