Tseketseke a Laz abwera


Lazalo muliyenda

Atakhala kunja kwa Mwezi, kuombedwa mphepo zina mmizinda ya ku Kenya, America ndi UAE, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera afika kumudzi tsopano. Ndipo abwela ndi chithumba chimene chikuyembekezereka kuthetsa mavuto a kusowa kwa mafuta, kuzimazima kwa magetsi ndi chipwirikiti pa za chuma.

A Chakwera anachoka ku Malawi pa 12 Mwezi watha kupita ku dziko la America ku msonkhano waukulu wa UN. Asanakafike ku America, iwo anaima ku Kenya kumene anakhala nawo pa mwambo olumbiritsa a William Ruto.

A Chakwera anali mtsogoleri oyamba kufika ku Amereka popitila msonkhano wa UNGA. Iwonso anali omalizira kuchokako.

Pa msonkhano wa UNGA, a Chakwera anauza atsogoleri ena kuti asiye kuonera mkodi Africa ndipo ayambe kuipatsa ulemu. Pamene atsogoleri ena anapotoloka kumapita kwawo, a Chakwera anatsalirabe ku Amereka. Mwa zina, iwo anakumana ndi a Malawi amene amakhala kumeneko. Iwonso anasayinira chithandizo cha ndalama zoposa 350 biliyoni Kwacha ndi dziko la Amereka.

Pamene amabwelera kumudzi, a Chakwera anadutsira ku dziko la United Arab Emirates kumene anawayimitsa kuti awamve chizungu chawo chotembenuza makosi. Mmalo mofika kumudzi kuno lamulungu, iwo afika lero.

A Malawi ambiri ali ndi chiyembekezo kuti kufika kwa a Chakwera kusintha zinthu pamene dziko lakumana ndi mavuto odabwitsa monga kusowa kwa mafuta nthawi imene anali kunja.

One comment on “Tseketseke a Laz abwera

  1. Where did you do your journalism?kuyankhula kwa bwanji kumeneko, let’s meet

Comments are closed.

Discover more from Malawi 24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading