Kubweretsa mafuta pa sitima yapamtunda kutha kupangitsa kuti mtengo utsike

Advertisement
Bungwe la Petroleum Importers Limited (PIL) lati kuyamba  kubweretsa mafuta pa sitima yapamtunda kutha kupangitsa kuti mtengo wamafuta utsike m’dziko muno.

Mkulu wa kampani ya Petroleum Importers Limited m’dziko muno a Martin Msimuko ndiwomwe anena idzi poyankhula ndi Malawi24.

A Msimuko ati kubweretsa mafuta pa Sitima yapa njanji ndikothandiza kwambiri chifukwa mafuta amabwera ochuluka nthawi imodzi ndipo izi zimapangitsa kuti mtengo wagulitsira utsike.

Iwo ati m’mbuyomu zakhala zikuchitika kuti mafuta amakhoza kukwera mtengo ndipo amathanso kuwatsitsa mtengo potengera ndimomwe akugulidwila kunja komanso kuyerekeza ndi ndalama ya dziko lino ndi ndalama yaku America.

Iwo adawonjezera kunena kuti njira zonse zobweretsera mafuta m’dziko muno zikhala zikugwira ntchito.

Msimuko

“Njira zonse zobweretsera mafuta m’dziko muno monga kubweretsa mafuta kuchokera ku Beira ndi Dar es Salaam kudzera pamagalimoto komanso kudzera ku doko la Nacala kudzera pa Sitima yapa njanji zikhala zikugwira ntchito,” adatero a Msimuko.

Iwo adatinso nkhokwe zosungira mafuta zilipo zokwanira koma kusowa kwa ndalama zakunja monga zaku America zikupangitsa kuti pakhale vuto lakagulidwe kamafuta.

Dziko la Malawi lakhala likuyitanitsa mafuta kudzera ku Beira ndi Darsalaam kudzera pamagalimoto koma tsopano layambanso kubweretsa mafuta kuchokera ku doko la Nacala kudzera pa Sitima yapa njanji.

 

Follow us on Twitter:

Advertisement