Chakwera atuma Joyce Banda ku maliro

Advertisement

Mtsogoleri wakale wa dziko lino Dr Joyce Banda wanyamuka lero kupita mdziko la Kenya komwe watumidwa ndi a Lazarus Chakwera kukawaimilira pa maliro a mtsogoleri wakale wa dzikolo a Mwai Kibaki.

A Kibaki omwe anali ndizaka 90, anamwalira lachinayi sabata yatha pa 21 April ndipo thupi lawo likuyembekezeka kulowa mmanda loweluka lino pa 30 April.

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera watuma mtsogoleri wakale wa dziko lino a Joyce Banda kuti ndiwomwe akawaimilire kumwambowo.

A Banda akuyembekezeka kukakhala nawoso pa mwambo okhuza omwe uchitike lachisanu lino pa 29 April ndipo uchitikira pa bwalo la masewero la Nyayo mumzinda wa Nairobi mdzikolo.

Poyankhula kwa atolankhani pomwe amanyamuka pa bwalo la ndege la Kamuzu ku Lilongwe, a Banda ati ndiwosangalala popasidwa mwai kuti akayimile mtsogoleri wa dziko lino ku maliloku.

Iwo ati a Kibaki omwe anabwerapo mdziko muno nthawi ya ulamuliro wawo, anali munthu wamasomphenya amene anatukula ntchito zamisewu komanso maulendo a sitima zapa mtunda.

A Banda anatiso adzawakumbukira a Kibaki kaamba koti ulendo omwe anabwera mdziko muno, anakhazikitsira limodzi ntchito yomanga mseu woyambukira (bypass) mumzinda wa Lilongwe.

Izi zikubwera pomwe mwezi watha, a Chakwera anatumaso mtsogoleri wakale wa dziko lino Dr Bakili Muluzi ku mwambo wa maliro wa mtsogoleri wa kale wa dziko la Zambia a Rupiah Bwezani Banda.

Advertisement