Pemphero Mphande ndi ine tili pa ubwezi – watsindika Keturah

Advertisement

Mtsikana odziwika ndi luso lokalasa nsambo komanso kuimba chamba cha Afro-Pop kuno ku Malawi, Keturah, watsimikizira onse omutsatira kuti iye ali pa ubwenzi ndi Pemphero Mphande.

Mu uthenga wake kudzera mu kanema ozijambula yekha yemwe wapereka kwa onse omutsata pa omutsatira lake la mchezo la Facebook mu usiku wa pa 20 April 2022, mtsikanayu anati wafuna kuwulula zoona  zokhudza iye ndi Pemphero Mphande yemwe ndi m’modzi mwa anthu odziwika bwino pa tsamba la Facebook.

“This is your local Girl Ketura, and I am here to tell you the truth about Pemphero Mphande, listen Pemphero Mphande and I are dating (Ine ndi ketura wanu wakomkuno kumudzi, ndipo ndili pano kuti ndikutsindikireni zoona zokhudza Pemphero Mphande. Tcherani philikanilo, Pemphero Mphande ndi ine tili pa Chibwezi ndithu),” anatsindika Ketura polankhula.

Mawu a oyimbayu adza maka patamveka manong’onong’ono pa masamba a mchezo kuti awiriwa akhala akuzemberana zodziwika koma iwo amazemba kulankhulapo pa za izi.

M’masiku apitawa, Pemphero Mphande yemwe adalinso omuongolera Keturah adati iye tsopano wasiya kukhalanso omuongolera m’mayimbidwe ake.

Maganizo a anthu ena ati Keturah wadya mfulumila kulengeza za ubwenziwu, ndipo akadayembekeza kuti Pemphero Mphande ndiye akhale patsogolo kuvundukula ku gulu za ubwezi wawo wamseliwu.

Pakadali pano, Mphande sadatsilirepo mlomo pa zomwe bwezi lake layankhula ku mtundu wa omukonda ndi kumutsata oyimbayu.

Keturah ndi  m’modzi mwa oyimba omwe  ndi odziwika bwino  m’Malawi maka kamba ka mawu ake a Nthetemya komanso luso lake lokalasa Nsambo lomwe adaphunzitsidwa ndi amalume ake m’mbuyomu. Iye wayimbapo nyimbo monga “Khalidwe ndi Chuma” komanso “Chembe”.

Advertisement