CDEDI yati ana asabaidwe katemera wa Korona popanda chilolezo cha makolo

Advertisement

Bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI) lachenjeza aphunzitsi onse komanso ogwira ntchito za umoyo kuti apewe kunyengelera ana asukulu kuti abayitse katemera wa Korona popanda chilolezo cha makolo.

Bungweli lanena izi muchikalata chake chomwe lalemba lero ndipo wasainira ndi Mkulu wa bungweli Sylvester Namiwa.

A Namiwa apempha ogwira ntchito za umoyo kuti azibaya ana okhawo omwe avomereza kuti abayitse katemerayu mwakufuna kwawo, ndipo pamene akukabayitsa akhale ali ndi makolo awo, kapena munthu aliyense amene amakhala ndi anawo, chifukwa kubaya katemera mokakamiza ndikuphwanya ufulu wa munthu.

Iwo ati chenjezoli likubwera potsatira kutsegulira kwa gawo lachiwiri la katemerayu ku Nsalu m’boma la Lilongwe sabata ino.

“Ogwira ntchito ku bungwe la CDEDI akhala akutsatira mwachidwi zomwe zikuchitika mdelari, ndipo adawona kuti ana oposa 100 adabayitsa katemerayu popanda makolo awo kapena owayang’anira.

“Ndizomvetsa chisoni kuti anawa akubayitsa katemerayu pongowafunsa pakamwa chabe ngati anawo anakawauza makolo awo kuti akufuna kubayitsa,” a Namiwa anatero.

Mkuluyu adatinso chokhumudwitsa nchakuti ana ena akubayitsa katemerayu chifukwa cha chibwana kapena kukopeka ndi anzawo.

Potero, akumbutsa kuti katemera wa Korona akufunika munthu wokhwima nzeru kuti apange chiganizo chofuna kubayitsa kapena ayi.

Malingana ndi a Namiwa, ana alibe kuthekera koganiza mokhwima nzeru chotere, nchifukwa chake akuyenera kuthandizidwa ndi makolo awo popanga chiganizo chimenechi ndipo makolo akuyenera kukhalapo pamene anawa akubayitsa katemerayu.

“Ndizodabwitsa kuti boma la Malawi likukakamira kupereka katemerayu kwa ana pamene umboni owonekeratu ulipo  wakuti nthendayi sikupereka chiwopysezo kwa ana.

“Pachifukwa ichi tikupempha boma kuti lisiye kumangotsanzira njira zopewera nthendayi zomwe zilibe nfundo zogwirika pa sayansi komanso zosagwirizana ndi zofuna za nzika za dziko lino,” anatero a Namiwa.

Namiwa watinso nzodabwitsa kuwona maboma akugwiritsa ntchito njira za utambwali pofuna kukakamiza ana ovutika komanso osowa omwe chofuna chawo ndi chakudya chopatsa thanzi komanso kutetezedwa ku nsinga za umphawi.

Iwo ati pakadali pano pali umboni kuti kukakamiza anthu kumakhala mu m’bindikiro komanso kuletsa anthu kuyendayenda kwawononga chuma cha dziko lino ndipo kwapha anthu ambiri kuposa nthendayi.

Advertisement